MkwasoUncategorized

Khansa ikusautsa anthu achialubino

Wolemba: Godfrey Maotcha

Kondowe: Ambiri safikira thandizo

Pomwe zimaoneka ngati vuto lakuphedwa kwa anthu akhungu la chialubino ndi lomwe linatenga malo masiku ammbuyomu, vuto la khansa ya pakhungu likubwe-retsa chiopsezo pa umoyo wa   anthuwa.

Malinga ndi mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la anthu akhungu la chialubino kuno ku Malawi, la  Association of People living with           Albinism (Apam) a Overstone Kondowe, anthu ambiri akuvutika kupeza thandizo.

“Kuyambira mwezi wa Malichi anthu akhungu la chialubino akhala akugwiritsa ntchito mafuta okutha mphamvu. Zotere zakhala zikubwe-retsa mavuto osaneneka pa umoyo wao,” anatero a Kondowe.

Zimenezi zikuchitika chonsecho nthambi ya boma yosunga mankhwala ya Central Medical Stores Trust ili ndi mankhwalawa koma m’zipatala za m’maboma mulibe.

Iwo ati bungwe lawo likuchititsa mikumano ndi nthumwi za boma kuti papezeke mafuta apadera othandiza khungu la chialubino. Mwa zina a Kondowe akufuna kuti mankhwala ndi mafutawa zidzipangidwa m’dziko muno.

Wothandizira mkulu woona za mankhwala ku Central Medical Stores Trust a Joe Khalani, anati bungwe lawo limatumiza uthenga ku ofesi wa zaumoyo m’maboma, kudziwitsa   ofesizi za mankhwala omwe bungweli liri nawo Lachisanu lirilonse.

Woyang’anira bungwe la Standing Voices kuno ku Malawi a Bonface Massah wati bungwe lake likuyesera njira zamakono zotetezera khansa ya pakhungu ndipo ati ali ndi chiyembekezo kuti boma livomereza njirayi.

Malinga ndi bungwe la United Nations khansa ya pakhungu ikupha anthu a khungu la chialubino muno mu Afrika kuponsa vuto lina lirilonse.