MkwasoUncategorized

Mfumu idzipha podziponya pa msewu

Adadzipha moziponya ku galimoto

Wolemba: Lawrent SANGWANI, Mtolankhani Wapadera

Mfumu ina m’boma la Thyolo yazipha poziponya pa msewu ndikugundidwa ndi galimoto lomwe likukonza msewu wa Makwasa-   Thekerani m’bomali

A Bornface Mathiya a zaka makumi anayi (40) omwe amacho-kera m’dera la Thekerani Mfumu Yaikulu Tsabwe m’bomali anachita izi ati kusatira kupha mkazi wao yemwe amamukaikira kuti amamuyenda njomba pomazemberana ndi amuna ena m’deralo. Mmene mkuluyu ankapha mkazi wake samadziwa kuti akuonedwa ndi ana ena omwe adali pafupi ndi malowa.

A Mathiya adazizimuka kuona gulu la anthu omwe adakhamukira komwe iye adali ndipo adazindikira kuti anthuwo akufuna iye polingalira zomwe wachita popha mkazi wake pomubaya ndi mpeni.

Pamenepo mkuluyu adaliyatsa  liwiro kuthawa khamuli koma atazindikira kuti sakwanitsa kuthawa gululi adaganiza zoziponya pa msewu pomwe pamadutsa galimoto lokonza msewuwo ndipo galimotolo lidavulaza ndi kupha a Mathiya.

Pamene apolisi a ku Thekerani amafika pa malopa adapeza mkuluyu atamwalira kale. A Mathiya asiya ana anayi ndi zidzukulu zitatu.