Bushiri wapempha abizinezi atsitse mtengo wa chimanga
Wolemba: Precious MSOSA
Pulofeti Shepherd Bushiri wapempha ogulitsa chimanga m’dziko muno kuti aganizire kutsitsa mtengo wa chimanga kuti anthu ambiri akwaniritse kugula ndi kukhala ndi chakudya.
Mneneri wa Bushiri a Ephraim Nyondo amalankhula izi pa mwambo wogulitsa chimanga chotsika mtengo kwa anthu ovutikitsitsa m’boma la Balaka masiku apitawa. A Nyondo anati Pulofeti Bushiri adaganiza zoyambitsa ntchito yapaderayi ataona kuti anthu ambiri akulephera kugula chimangachi.
“Chimanga chilipo chambiri koma anthu akulephera kugula chifukwa ndichokwera mtengo kwambiri. Ichi ndichifukwa Pulofeti Bushiri anaganiza zoyambitsa ntchito yogulitsa chimangachi kuti anthu a m’maboma osankhidwa apindule nawo,” anatero a Nyondo.
Iwo anati atafikira m’maboma asanu ndi awiri, anthu ambiri akufunitsitsabe chithandizochi m’madera ena. Iwo amagulitsa thumba la makilogalamu 25 pa mtengo wa K2,500 ndipo amwayi amatha kugula matumba awiri. Pa msika thumba la makilogalamu 50 pakadalipano likugulitsidwa pa mtengo wa K18,000.
“Ndife okondwa kuti anthu akutipempha kuti tipitirize kotero tiyesetsa kuti tifikire paliponse ndicholinga chowonesetsa kuti pakhomo paliponse pali chakudya. Komabe ndipemphe akufuna kwa-bwino makamaka mabungwe ndi boma kuti tiwathandize anthu athu kukhala ndi chakudya,” anatero a Nyondo.
Pa mndandanda wa maboma omwe amayenera kuthandizidwa ku chimanga chotsika mtengochi, boma la Balaka panalibepo ndipo zinachita kutengera phungu wakale wa dera la kumpoto kwa bomali a Lucius Banda kupempha kwa a Bushiri.
“Nditawona momwe anthu makamaka azimayi amavutikira pa msika wa Admarc kwa Sosola kudikirira kugula chimanga cholemera makilogalamu khumi zinandikhudza kwambiri. Uwu unali umboni woti anthu ambiri akusowekera chimanga choncho ndichifukwa ndinapempha a Pulofeti athu a Bushiri kuti aganizire kugulitsanso chimangachi ku Balaka kuno,” anatero a Banda.
Iwo anati si kuti akuchita izi ndi malingaliro odzaimiranso uphungu koma kuti ndi mtima chabe wongofuna kuthandiza ena omwe akusowekera. Matumba 1,200 ndiomwe anagulitsidwa m’bomali.
Ena mwa maboma omwe Pulofeti Bushiri anafikira ndi chimanga chotsika mtengo ndi Ntcheu, Salima, Mzimba, Phalombe, Thyolo ndi Mangochi.
Can you be more specific about the content of your article? After reading it, I still have some doubts. Hope you can help me.