KOMITI YA ZACHUMA IKUGONA TULO
Wolemba: Precious MSOSA
Lipoti lounika kagwiritsidwe ntchito ka ndalama za boma lomwe bungwe la OXFAM linachita lati kuchedwa kwa komiti yoona zachuma cha boma ya ku Nyumba ya Malamulo ya Public Accounts Committee (PAC) kuzukuta malipoti a mkulu wa ofesi yowunika ndalama za boma (Auditor General) kukupereka danga lowononga ndalama za boma.
Malingana ndi lipotili, lomwe linatulutsidwa m’chaka cha 2018 mogwirizana ndi bungwe la Integrity Platform, komiti ya PAC siyinawunikirebe malipoti oyambira m’chaka cha 2013 mpaka 2016 omwe ofesi ya Auditor General inapereka ku Nyumba ya Malamulo.
Mwazina, ofesi ya mkulu wowunikira chuma cha boma imapanga malipoti a momwe chumachi chagwiritsidwira ntchito ndi nthambi za boma komanso maofesi ena pofuna kuwonesetsa kuti omwe apezeka kuti asakaza chumachi azengedwe mlandu.
Lipotili lati ngakhale pali kusintha kwakukulu kuchokera ku ofesi ya mkulu wowunikira chuma cha boma pa ntchito yomaliza ndi kupereka malipotiwa ku Nyumba ya Malamulo, kuchedwa kwa komiti ya PAC kuchitapo kanthu kukubwe-zeretsa mmbuyo cholinga cha ofesiyi.
“Pali umboni waukulu woti ntchito yowunikira ndalama za boma siyingamakwaniritse cholinga chake chomwe ndikuteteza chuma cha boma,” likutero lipotilo.
Mwa chitsanzo, mu lipoti la m’chaka cha 2016, ofesi ya mkulu wowunikira ndalama za boma linapeza kuti ndalama pafupifupi K225 miliyoni zinasokonekera mu Unduna wa za Malimidwe, Ulimi wa Mthilira ndi Chitukuko cha Madzi. Koma mpaka pano komiti ya PAC siyinagwirepo ntchito pa lipotili.
Malinga ndi lipoti la OXFAM, komiti ya PAC ikawunguza malipoti ochokera kwa Auditor General ndipo yanunkhiza kuti pena pake panachitika za chinyengo pa kagwiritsidwe ntchito ka ndalama. Iyo imalumi-kizana ndi bungwe lothana ndi katangale la Anti Corruption Bureau (ACB) kuti lipitirize nkhaniyo powatsegulira mlandu.
Koma poyankhapo pa chifukwa chomwe komiti ya PAC imachedwera kuwunikira mali-potiwa, wapampando wa komitiyi a Ken Kandondo anati nthawi zambiri izi zimakhala chonchi chifukwa chakusowa kwa ndalama zomakhalira ndi mikumanoyi.
Koma iwo anati kuchedwa ndikobwezeretsa mmbuyo nkhani yowonesetsa kuti ndondomeko za katetezedwe ka chuma kakutsatiridwa.
A Kandodo anavomereza kuti komiti yawo yapezadi milu ya malipoti ochokera m’zaka za m’mbuyomu koma anati achita chotheka kuti awamalize msanga. Iwo anati pakadali pano akuyembekezeka kuyamba kuwunika lipoti la m’chaka cha 2019.
Your article helped me a lot, is there any more related content? Thanks!