General

Mabanja 1,408 alandira thandizo la chakudya ku Balaka

Wolemba: Joseph KAYIRA

Boma lathandiza mabanja 1,408 ochokera m’dera la ku zambwe kwa Balaka, omwe alandira chimanga, nyemba komanso mapulasitiki okungira madenga a nyumba zawo kaamba koti mphepo ya mkuntho ya Chido kudzanso ya namondwe wa Freddy m’mbuyomo – kuphatikizapo kusintha kwa nyengo, zaononga kwambiri kumeneko ndipo anthu akusowa mtengo wogwira.

Polankhula pa mwambo wopereka katunduyu kwa ena mwa mabanja okhuzidwa, pa mwambo omwe unachitika Lolemba pa 23 Disembala 2024, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Dr Michael Usi, anati boma la Malawi ndilokhuzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi zomwe zakhuza maboma ambiri, kuphatikizapo Balaka.

Dr Usi: Boma lifikira onse amene akhuzidwa ndi vutoli

Iwo anati thandizolo labwera kaamba ka pempho lomwe phungu wa Nyumba ya Malamulo wa dera la ku zambwe kwa boma la Balaka, a Bertha Ndebele, anapereka ku ofesi kwawo.

“Munthu akamanena zoona amaoneka. Wolemekezeka a Ndebele atadandaula za vuto lomwe liri kuno amaonekeratu kuti akunena zoona. Titakambirana ku boma tinachiona chinthu chofunikira kuti tithandize mabanja okhuzidwawa. Tikudziwa kuti pali ena ambiri amene sitinawafikirebe ndipo kubomako tikuyesetsa kuti tifikire onse amene akhuzidwa ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi posaona chipani, chipembedzo kapenanso mtundu wa munthu,” Dr Usi anatero.

Dr Usi kupereka chimanga kwa m’modzi mwa okhuzidwa

Dr Usi anapempha onse amene akukhuzidwa ndi ntchitoyi kuti akhale ndi umunthu pogwira ntchitoyi mwachilungamo kuti thandizoli lifikire ovutikawo. Iwo anachenjza kuti amene akugawa chakudyachi ndipo sakutsata malamulo “sakupempha china koma kuchotsedwa ntchito.”

“Sitikuchita ndale koma kuthandiza anthu amene akhuzidwa. Vutoli likusowa kuti tichite chilungamo. Ndale sitichita ndi munthu wa njala. Tikhale ndi chifundo komanso kutsogoza Mulungu pa ntchitoyi. Ife ngati boma, takangalika kukafika paliponse kuti tithandize omwe akhuzidwa ndi vuto la njala komanso la ngozi zogwa mwadzidzidzi,” anatero Dr Usi.

Ndipo mu mawu awo, a Ndebele anati kwa zaka zitatu tsopano, anthu a m’dera lawo akhala akuvutika pa nkhani ya chakudya chifukwa cha ng’amba. Iwo atinso namondwe wa Freddy, komanso Chido, anakolezeranso kwambiri mavuto amene anthu akukumana nawo m’dera lawo.

Ndebele: Sindinachitire mwina koma kuthamangira ku boma kuti atithandize

“Anthu akugona ndi njala m’dera langa ndipo ndinachiona chanzeru kuti ndikagwade ku boma komwe sanachedwetse koma kundithandiza. Ndikuthokoza mwapadera ku boma chifukwa chondithandiza mwa msanga. Ndikungopitiriza kunena kuti vutoli ndilalikulu ndipo pali mabanja ambiri amene akhuzidwa. Akufuna kwabwino asatope ndi kutithandiza,” a Ndebele anatero.

Iwo anati anthu a m’dera lawo amachilimika pa ulimi ndipo akhala akuchita ulimi wanthirira koma zinthu zingasinthe atathandizidwa ndi mapampu kuti azitha kuthirira mbewu zawo mosavuta.

“Ulimi wodalira makeni ndiovuta; anthu akufuna makina monga mapampu kuti azitha kuthirira malo aakulu. Tikulimbikitsa kuti anthu asamangodalira ulimi wa mvula wokha ayi. Choncho atithandize ndi mapampu ndipo ndikukhulupirira kuti njala idzachepa,” anatero a Ndebele.

M’modzi mwa anthu amene alandira nawo katunduyu, a Margret Masitala, a m’mudzi mwa Mwelero, kwa Mfumu Yaikulu Nsamala ku Balaka, anati ndiokondwa kuti banja lawo tsopano lawona kuwala “chifukwa likadya”.

Mfumu Nsamala inathokozanso boma chifukwa cha thandizolo

“Ndikuthokoza Pulezidenti [Lazarus] Chakwera chifukwa chotikumbuka pamene tikudutsa mu nyengo zovuta. Tilipo ambiri ndipo tilinso ndi chikhulupiriro kuti atifikira tonse. Tinavutika kwambiri ndi namondwe wa Freddy; apanso kunabwera Chido, komanso ng’amba yomwe yatisautsa kwa zaka zitatu. Tisowabe thandizo ndithu,” anatero a Masitala.

Ena mwa omwe anathokoza boma kaamba ka thandizolo ndi mkulu wa nthambi ya boma ya Department of Disaster Management Affairs (DODMA), a Charles Kalemba, Bwanamkubwa wa boma la Balaka, a Tamanya Harawa ndi Mfumu Nsamala.

Masitala: Atipulumutsa ku njala

Malingana ndi malipoti, boma la Balaka linalandira mphepo yamphamvu mu mwezi wa Novembala yomwe idagwetsa ndi kusasula madenga a nyumba zambiri. Panthawiyo, mabanja okwana 2,604 anakhuzidwa ndipo ndi ochokera m’madera a mafumu osiyanasiyana m’bomali.

Nthambi ya DODMA yakhala ikutsogolera ntchito yothandiza okhuzidwa ndi nyengo ya El Nino yomwe yakhuza kale mabanja 51,802. Mabanjawa ayamba kale kulandira chimanga. Nyengo ya El Nino imakhuza kabweredwe ka mvula ndipo siigwa mokwanira, zomwe zimakhuzanso zomwe alimi amakolola.