Woimba anjatidwa chifukwa chothawitsa buthu
Apolisi ku Mangochi amanga Abdul-Karim Saidi pa mlandu wothawitsa mtsikana wachichepere wa zaka 14 wa fomu 2 m’bomali.
Mneneri wa apolisi ku Mangochi a Amina Tepani Daudi atiuza kuti Saidi yemwe amatchuka ndi dzina loti Bandera pa nkhani ya maimbidwe anapanga izi pa 2 Janyuwale 2025.
Iwo ati pa tsikulo, Saidi atamutenga pa galimoto mtsikanayu anazungulira naye m’malo osiyanasiyana pa boma kenako ndikupita naye ku nyumba kwake.
“Koma atafika kunyumbako, mtsikanayu anakana kugona kotero Saidi anaganiza zopita ku malo ogona alendo komwe anakakhala naye masiku awiri,” atero a Daudi.
Iwo ati amayi a mwanayu anayesera kumuyimbira foni yake koma samayankha. Koma iwo apitiriza kuti ali ku malo ogona alendoko, mtsikanayu anamuwuza Saidi kuti akufuna kumapita kwawo.
“Zitatero, Saidi anawayimbira foni mayi a mtsikanayu kuti asadandaule za mwana wawo. Apa ndipomwe mayiwa mogwirizana ndi achibale anagwirizana ndi Saidi kuti akumane pena pake ndipo iye anavomera kenako atakumana amayi akewo anakampereka ku polisi,” iwo anatero.
Koma mtsikanayu atamufunsa, iye anawulula kuti palibe zogonana zomwe zinachitika chifukwa anali akusamba. Pakadali pano apolisiwa adakali kudikira zotsatira.
Koma a Daudi anati atamufunsa Saidi zomwe amapanga ndi mtsikanayu, iye anati amafuna kujambula kanema wa nyimbo yake.
Saidi amachokera m’mudzi mwa Kalonga mfumu yayikulu Mapira m’bomali