Mkwaso

Ngalande wakangalika kutukula amayi, achinyamata pa bizinesi

Wolemba: Joseph KAYIRA

Phungu woima payekha wa Dera la Kumpoto kwa Balaka, a Tony Ngalande ati ndi cholinga chawo kuti amayi ndi achinyamata atukuke pa bizinesi zing’onozing’ono zomwe akuchita m’makomo mwawo pofuna kuthandiza kuchepetsa umphawi mogwirizana ndi ndondomeko za boma la Malawi [Malawi2063) komanso za bungwe la maiko onse [United Nations] za chitukuko za Sustainable Development Goals [SDGs]. Mwa zina, mfundozi zikulimbikitsa ntchito zolimbana ndi umphawi, kuthana ndi njala, kulimbikitsa umoyo wabwino kwa onse komanso kuti anthu azichita zitukuko zosiyanasiyana.

Polankhula ku Balaka Loweruka pa 1 February 2025 pomwe amapereka ndalama zokwana K24 miliyoni kwa magulu 60 abizinesi omwe muli amayi ndi achinyamata, a Ngalande anati ndiokondwa kuti tsiku ngati ili lafika ndipo akwaniritsa zomwe analonjeza masiku apitawa.

Iwo afotokoza kuti pali amayi ambiri amene akuvutika koma amatakataka kuchita bizinesi. A Ngalande ati amayi amenewa kudzanso achinyamata akuyenera kuthandizidwa moyenerera kuti mabizinesi awo apite patsogolo komanso miyoyo ya m’mabanja awo ifike pabwino.

“Ngongole zimene tikuperekazi ndi zabwino chifukwa cholinga chake ndi kusintha miyoyo ya anthu. Tapereka K400,000 ku gulu lirilonse ndipo izi zikutanthauza kuti pagulu membala azilandira K20,000. Ndi ndalama imene yabweretsa chimwemwe pa nkhope za anthuwa chifukwa ithandiza kutukula mabizinesi awo – kaya ndi a mandazi, ogulitsa masamba – ndi zina zotero,” anatero a Ngalande.

Phunguyu anati popereka ngongole saukuona nkhope kuti munthu wachokera chipani chiti koma kuti akufuna kuthandiza aliyense “chifukwa ine ndi phungu wa aliyense; aliyense amandivotera.”

A Ngalande ati ali ndi chikhulupiriro kuti maguluwo agwiritsa ndalama moyenerera kaamba koti anthuwo akudziwa ululu wa umphawi. Iwo afotokoza kuti akukhulupiriranso kuti anthuwo achita chotheka kuzabweza ngongoleyo kuti enanso apindule nawo.

Phunguyu wati ndicholinga chake kuthandiza anthu ochuluka ndipo pali magulu 100 omwe akufuna kuti awafikire ndi ngongoleyo ndipo mwa awa, 60 alandira kale ndalama.

M’modzi mwa anthu amene apindula ndi ngongoleyo, a Maria Henderson, a zaka 39 omwenso ali ndi ana anayi, a m’mudzi mwa Kaumphawi 1, mfumu yaikulu Nsamala m’bomalo, ati ndiokondwa kwambiri kuti loto lawo loyambitsa bizinesi latheka.

Iwo afotokoza kuti gulu lawo, la Chikondi Alinafe, liri ndi malingaliro oyambitsa bizinesi monga kugulitsa tomato komanso kumanga majumbo a makala.

“A Ngalande achita zitukuko zosiyanasiyana kuno ku Balaka, sitingakwanitse kutchula zabwino zimene amachitira anthu. Ndalama imene talandirayi isintha miyoyo yathu chifukwa tizikhala ndi ndalama nkumagula zosowa pa moyo wathu. Ife tinalibe chochita koma tsopano pano tikuyenda ndi mdidi chifukwa a Ngalande atiwombola mu umphawi,” anatero mayi Henderson.
A Henderson afotokoza kuti kuyambira chaka cha 2019, pomwe a Ngalande anatenga udindo wa Phungu wa Dera la Kumpoto kwa Balaka, phunguyu wakhala chitsanzo chabwino cha momwe phungu akuyenera kuchitira ku dera lake ndipo zina mwa izo ndi ndalama za ngongole akupereka potukula amayi ndi achinyamata.

Pali chiyembekezo choti a Ngalande adzapikisana nawo ngati phungu wa Nyumba ya Malamulo mu dera latsopano la Balaka Ngwangwa pa chisankho chimene chichitike pa 16 Sepitembala chaka chino. Madera ena komwe amene akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa phungu ndi Rivirivi, Utale, Ulongwe komanso Bwaila.