Zigandanga zakuba K7 miliyoni ndi kulanda mfuti zigwidwa ku Lilongwe
Polisi ya Lilongwe yati ikusunga mchitokosi anthu awiri powaganizira kuti ndi omwe amachita zaumbanda ku Admarc ya Kasiya kwa Malembo m’bomali komwe akuba anaba ndalama zokwana K7 miliyoni pa 29 Januwale 2025.
Malingana ndi mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu, anthuwa ndi a Maupo Chalemera a zaka 38 ndi a Innocent Banda a zaka 29.
A Chigalu ati patsikulu, gulu la akuba linapita ku Admarc imeneyi ndi kumumanga mlonda komanso kuba mfuti yake kenako anathyola chitseko cha ofesi ya yemwe amawona ntchito za malonda ndikuba ndalama zokwana K7 miliyoni.
A Chigalu ati kutsatira kafukufuku wa apolisiwa, iwo amanga a Chalemera ku Kasiya ndi a Banda kwa Mtsiriza komwe amakhala.
Iwo ati atawafunsa, awiriwo anavomera kuti amachitadi zaupanduzi ndi kuwalondolera apolisiwa ku manda komwe anabisa mfutiyo.
Pakadali pano a Chigalu ati apolisiwa akusakasaka anthu ena asanu omwe anali gulu la anthu akubawa.
Awiriwa akawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu wakuba.