Ngalande walonjeza zobweretsa zitukuko zochuluka

Mbali ina ya chipatala cha Khwisa (Chithunzi: Joseph Kayira)
Wolemba: Joseph KAYIRA
Phungu wa Dera la Kumpoto kwa Balaka a Tony Ngalande — omwenso amadziwika kuti Pulezidenti wa Balaka — ati abweretsa zitukuko zosiyanasiyana m’bomali atakhutira ndi zitukuko zomwe zatheka kale mdera lomwe amaimira ku Nyumba ya Malamulo ndi madera ozungulira.
A Ngalande amalankhula izi pomwe amakayendera ina mwa mijigo yomwe tsopano anthu akugwiritsa ntchito m’madera a Khwisa ndi Matola mongotchulapo ochepa. Iwo akwanitsanso kukonza mipope imene inali yoonongeka ndipo pano anthu ochokera mu nyumba zochuluka akumwa madzi aukhondo. Pakali pano mipope 400 ikugwira ntchito.

Ngalande: Zomwe ndinalonjeza ndikukwanitsa (Chithunzi: Joseph Kayira)
“Ndakwanitsa zomwe ndinalonjeza kwa anthu anga. Chizindikiro changa ndi mjigo ndipo sindikuchitanso kampeni koma kungowafunsa anthu kuti kodi zimene ndinalonjeza ndakwanitsa? Chachikulu chomwe ndinawalonjeza anthu ndi madzi ndipo madziwa tsopano ali ponseponse,” anatero a Ngalande.
Phunguyu anati, kudzera mu ubale wake wabwino ndi bwingwe lina, wakwanitsa kukumba mijigo yochuluka kuti anthu azimwa madzi aukhondo chifukwa izi zimathandiza kuchepetsa matenda monga kolera ndi ena.
“Tisanabweretse chitukuko chimenechi, amayi amatha kuyenda mtunda wa makilomita asanu kapena kupitirira apo kusaka madzi. Tinagwirizana ndi bungwe lina la Chisilamu lomwe linatithandiza kukumba mijigo ndipo pano zinthu zili bwino. Sindisiyira pompa ayi. Pali zitukuko zambiri zomwe zikubwera kutsogoloku. Cholinga changa ndi kusintha Balaka kuti afike pabwino,” anatero a Ngalande.

Kusangalala kuti madzi afika m’mudzi (Chithunzi: Joseph Kayira)
A Ngalande anayenderanso chipatala cha Khwisa chomwe pakali pano chatsala pang’ono kuti achimalizitse kumanga. Iwo ati kwa zaka zingapo ntchito inayima pachipatalachi koma atasankhidwa ngati phungu, iwo anachita chotheka kuti boma lipereke ndalama zomalizitsira kumanga chiptalacho.
“Kuchoka 2014 mpaka 2019 ntchito yomanga chipatala cha Khwisa inaima. Koma kuchoka 2020 kufika pano ndachita chotheka kuti zinthu ziyambenso kuyenda. Pakali pano ntchito ili mkati pa chipatalachi. Ndikuthokoza boma potipatsa ndalama kuti ntchitoyi itheke.
“Chipatalachi chikatha padzakhalanso nyumba ya chisoni ndipo anthu sadzidzavutika monga m’mene zimakhalira pano zikationekera chifukwa anthu amapita komwe ku chipatala cha Balaka. Zambiri zizichitikira pa chipatala pompa. Tikatero tichepetsa ntchito yambiri yomwe imakhala ku chipatala chachikulu; komanso anthu samayenda mtunda wautali kukafuna thandizo la chipatala,” anatero a Ngalande.

Gulupu Mackenzie: Anthu ochokera m’madera ena akusirira m’mene phungu wathu akuchitira zitukuko (Chithunzi: Joseph Kayira)
Phothirirapo ndemanga pa zitukuko zomwe zachitika mderalo, a Gulupu Mackenzie — omwe dzina lawo lenileni ndi a Idesi Kumtengo — anati ndiwokondwa kuti anthu tsopano ali ndi madzi otetezedwa bwino komanso aukhondo.
“Vuto la madzi lachepa kwambiri. Aliyense akumwa madzi aukhondo. Tinaiwala zotunga madzi mzithaphwi. Komanso ndife okondwa ndi momwe ntchito yomanga chipatala ikuyendera. Posachedwa tidzilandira thandizo la chipatala pafupi pompa,” anatero a Gulupu Mackenzie.
Malingana ndi kusintha kwa malire a madera a aphungu a Nyumba ya Malamulo, tsopano a Ngalande adzaimira Dera la Balaka Ngwangwa. Masiku apitawa phunguyu anagawa ufa, mabulangete, ndalama komanso mapulasitiki ofolera nyumba kwa anthu mderalo pa mwambo womwe unachitikira pa bwalo la Andiamo.
A Ngalande anati sawasiya okha anthu kuti avutike ndi njala ndipo achita chotheka kuti chakudya chigawidwe kwa onse amene ali pa chiopsezo cha njala.