A UN apempha kulolerana pakati pa zipembedzo
Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA
Mkulu woyang’anira ntchito za bungwe la United Nations (UN) kuno ku Malawi a Maria Jose Torres apempha Amalawi kuti alemekeze zikhulupiliro za zipembedzo ndi kukambirana mwa mtendere ngati akusemphana zikhulupiliro pothetsa kusamvana komwe ku-mabuka chifukwa chosiyana zipe-mbedzo.
Iwo anayankhula izi mchikalata chomwe bungweli linatulutsa kutsatira kusamvana komwe kulipo pakati pa akhristu ndi asilamu komwe kwabuka m’boma la Balaka. Kusagwirizanaku kwadza kutsatira mpingo wa Anglican kuletsa ophunzira achisilamu kuvala Hijab pa sukulu ya pulaimale ya Mmanga ndi sekondale yoyendera ya Mmanga. Hijabu ndi chomwe azimayi komanso atsikana achisalamu amavala kuzibisa kumutu, khosi komanso pachifuwa.
Kusagwirizanaku kunakula mpaka magulu awiriwa anayamba kumenyana ndi kuwonongerana zinthu komanso anthu ena kuvulala modetsa nkhawa.
Mchikalatachi a Torres akukhumudwa ndi zomwe zinachitikazi ponena kuti ndi zosaloledwa.
“Ufulu woyankhula ndi chipembedzo ndi nsanamira za demokalase,” anatero a Torres.
Iwo anati kuletsa munthu kupeza mwayi wa maphunziro chifukwa cha chipembedzo kapena zikhulupiliro ndi kuphwanya ufulu wa anthu potengera malamulo a zamaphunziro mmene alili mu gawo 36(3), (111) a 2013.
Nalo bungwe la Muslim Association of Malawi (MAM) kudzera mwa mlembi wamkulu a Alhaji Twaibu Lawe linatulutsanso chikalata chodzudzula zomwe zinachitikazi.