MkwasoUncategorized

Kuphana kwasokoneza Malawi

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA ndi Joseph KAYIRA

Pamene anthu akudikirira kuti amve zotsatira za mlandu wa chisankho cha pulezidenti womwe uli mkhoti pakali pano, akatswiri ena achenjeza kuti ziwawa zipitirira ngati atsogoleri apitirire kukulirana mtima ndikuika zofuna zawo patsogolo. Chichitikireni chisankho chachikulu pa 21 Meyi, m’dziko muno mwakhala muli kusamvana pakati pa chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) ndi Malawi Congress Party (MCP), United Transformation Movement (UTM) ndi mabungwe omwe siaboma omwe akusogozedwa ndi gulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC).

Pulezidenti Mutharika ndi atsogoleri a bungwe la mipingo la PAC akhala akukambirana za mtendere

Katswiri wina pa ndale yemwe anati tisamutchule dzina akuti Pulezidenti Peter Mutharika akuyenera ku-tsogolera pa ntchito yolimbikitsa umodzi komanso kukambirana ndi atsogoleri a zipani zotsutsa ndi mabungwe omwe siaboma.

Katswiriyu yemwe ndi mphunzitsi pa sukulu ina ya ukachenjede anati zomwe zikuchitika pakali pano monga kuphana, kuvulazana komanso kuotcherana nyumba ndi katundu zikupereka mantha kwa Amalawi ndi maiko ndi mabungwe omwe amagwirizana ndi dziko lino.

“Zoterezi zimakhudza ntchito zachuma, chitukuko komanso mte-ndere. Anthu amauzana kuti ku Malawi kulibe mtendere ndipo alendo omwe amabwera kudzayendera malo okongola a m’dziko muno amasankha kupita kumaiko ena,” anatero katswiriyo.

Masiku apitawa pulezidenti Mutharika wakhala akunenetsa kuti iye ndi amene adapambana pa chisankho cha pulezidenti ndipo ena amene akulimbana naye akungoye-nera kulolera zotsatira zachisankhozi. Koma pa msonkhano waposachedwapa womwe anachititsa pa bwalo la Gymkhana mu mzinda wa Zomba, a Mutharika anapempha atsogoleri azipani zotsutsa ndi mabungwe omwe siaboma kuti akhale ololerana ndikusiya mtima wa chimkulirano.

Iwo analankhula izi atamaliza kupereka ma satifikite kwa ophunzira 225 pa sukulu ya ukachenjede ya Chancellor. M’mawu awo a Muntharika anati kulolerana ndi njira yokhayo yomwe ingadzetse umodzi womwe pakali pano uli pa chiopsezo.

“Kuwononga zinthu, kuyenda ndi kupanga zionetsero m’misewu sizingapititse ntchito za chitukuko m’dziko muno patsogolo ayi. Komanso mabizinesi athu sangayende bwino ngati anthu akungokhalira m’misewu kuchita ziwonetsero. Tiyeni timange umodzi; tonse ndife Amalawi ndipo kusiyana zipani kusatipangitse kukhala anthu osalolerana,” anatero a Mutharika.

Koma katswiri pa ndale yemwe tinalankhula naye wati vuto la zonsezi ndi loti a Mutharika akungo-lankhulapo koma sachita zomwe anenazo. Iye wati Pulezidenti Mutharika ndi atsogoleri ena a DPP akhala akulankhula mokhadzula mmalo moluzanitsa Amalawi.

“Zomwe akunenazi ndi zapakamwa chabe osati kumanga umodzi. Akumati lero akamba izi mawa zina. Ngati akufuna azipani zotsutsa ndi amabungwe amange umodzi ndi boma la chipani cha DPP akuyenera kuyankhula mawu a mtendere m’misonkhano yawo osati kupanga zinthu zophwasula.

“Chisankho chikanayenda bwino bwenzi zonse zimene zikuchitika panozi kulibe. Koma kusafuna kugonjerana pakati pa andale ndi mkana dziko lino anthu akungopanga zionetsero kapena ziwawa m’mene afunira. Izi zikuchitika kaamba ka mkwiyo womwe anthu ali nawo,” anatero mkuluyu.

A HRDC akhala akuchititsa zionetsero zosakondwa ndi m’mene bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) linayendetsera chisankho cha pa 21 Meyi chaka chino. Bungweli likuti likufuna wapampando wa MEC mayi Jane Ansah atule pansi udindo wawo limodzi ndi makomishonala omwe adayendetsa nawo chisankhochi.

Mdziko muno mwakhala muli chimpwirikiti ndipo anthu ena ataya miyoyo yawo. Mwachitsanzo mnyamata wina yemwe amachita nawo zionetsero ku Karonga anamenyedwa ndi asirikali ndipo anamwalira ali m’manja mwa apolisi ku Mzuzu.

Ku Lilongwe anthu ochita zionetsero akhala akuvula komanso kumenya anthu ndikuononga katundu waboma komanso wa anthu mu dzina la kusakondwa ndi mmene zisankho zidayendera. Ku Lilongwe komweko wapolisi, a Usumani Imedi, anagende-dwa ndi anthu kwa Msundwe mpaka kuphedwa. Pakali pano apolisi awiri ndi amene anaphedwa pa ziwawa zofuna kuti mayi Ansah atule pansi udindo wawo.

Pali malipoti oti apolisi ena pokafufuza za kuphedwa kwa a Imedi nawo anamenya anthu ndi kugwiririra amayi ndi atsikana kumeneko. Akulikulu la apolisi analengeza kuti akhazikitsa komiti yomwe ikufufuza zankhanzazi. Mabungwe ena omwe siaboma nawo akuti afufuza bwino za zomwe zinachitika kwa Msundwe.

Kusalolerana kwasefukila kwa-mbiri pa nkhani zosiyanasiyana moti m’madera ena anthu akutengera lamulo m’manja mwawo. Posachedwapa ku Balaka akhiristu ndi asilamu anamenyana pa nkhani yokhudza chovala cha hijabu (ichi ndi chovala chomwe amayi ndi atsikana achisilamu amavala kumutu). Mpingo wa Anglican womwe umayendetsa sukulu ya M’manga m’boma la Balaka ukuletsa ana achisi-lamu kuvala hijabu ku sukulu.

Ku Neno nako kwakhala kukuchitika ziwawa kwa kanthawi tsopano. Posachedwapa ku Neno abambo awiri anaphedwa powaganizira kuti anali mfiti ndipo amakhuzidwa ndi imfa ya mnyamata wina kumeneko.

Ku Nkhata Bay anthu a midzi iwiri anavulazana ndi kuphana pa ziwawa zomwe zinathera ndi anthu anayi kuphedwa ndipo nyumba 21 kute-nthedwa.

Nyumba ndi galimoto za apolisi ndi anthu wamba zakhala zikutenthedwa maka mchigawo chapati ndi kumpoto komwe zionetsero zinakolera kwambiri. Masiku apitawa anthu aku Nsalu ku Lilongwe anatentha munthu wina yemwe amamuganizira kuti anabaya dalaivala wa taxi. Akuti wopalamulayo anatengedwa ndi dalaivala wa taxi kuchoka ku Lilongwe kupita ku Nsalu ndipo atafika kumeneko woganiziridwa uja anabaya ndi mpeni dalaivala wa taxi.

Dalaivala wa taxi atakuwa anthu a mmudzi anabwera kudzamuthandiza koma wachiwembu anali atathawa koma anaiwala foni yake ya m’manja. Foniyo ndi imene inamugwiritsa ndipo anthu a mmudzi anakhamukira ku nyumba kwake komwe anakatentha nyumba ndi katundu.

Woganiziridwa ataona kuti zathina anathamangira ku polisi kukazipereka koma khamu la anthu linalondola munthuyo ku polisi ndi kukamulanda mmanja mwa apolisi ndi kumutentha ndi moto. Mmene amafika naye ku chipatala munthuyo anali atamwalira. Apolisi apempha anthu kuti asamalange wokha akagwira woganiziridwa kuti walakwira lamulo.

A Henry Chingaipe, omwe amatsatira bwino nkhani za ndale m’dziko muno adauza nyuzipepala ya Nation on Sunday ya pa 10 Novembala 2019 kuti zonse zikuchitikazi zikuonetsa kuti anthu ataya chikhulupiriro pa ntchito zachitetezo komanso ntchito zachilungamo ndipo angoganiza zomatengera lamulo m’manja mwawo.

Iwo akuti mmbuyomu anthu amatsatira malamulo chifukwa boma limakwaniritsa kugwira ntchito yake bwinobwino, koma vuto lomwe lilipo ndiloti anthu ena akuganiza kuti awa amene ali m’boma sanapambane.

“Kusokonekera kwa zinthuku komwe kwachititsa kuti anthu atengere lamulo m’manja mwawo kwadza chifukwa anthu alibe chikhulupiriro ndi nthambi zomwe zinakhazikitsidwa kuti zidzithetsa kusamvana kukakhalapo,” anatero a Chingaipe mu nkhani yomwe nyuzipepala ya Nation on Sunday yasindikiza yotchedwa ‘Mayhem reigns’.

Apolisi akhala akunena kuti iwo ndiwokonzeka kugwira ntchito ndi anthu koma pena ntchito yawo imadzavuta chifukwa anthu ena aupandu amaotcha maofesi apolisi penanso kuwachita chipongwe apolisiwo.

Pakali pano bungwe la mipingo la Public Affairs Committee (PAC) lakhala likukumana ndi zipani ndi mabungwe omwe siaboma kuphatikizapo Pulezidenti Mutharika kuti pakhale kukambirana koona mtima momwe ziwawazi ndi kusakhulupirirana kungathere.

Ambuye Thomas Luke Msusa, Arkiepiskopi wa Arkidayozisi ya Blantyre, omwe omwe akuyesetsa kubweretsa pamodzi atsogoleri kuti akambirane zamtendere kudzera mu bungwe la PAC, anauza AMECEA   Online News kuti kulowererapo kwawo pa nkhaniyi kwathandiza kuti zipani zotsutsa zitenge njira yabwino yofuna kupeza chilungamo pa zomwe zinachitika pa chisankho cha pa 21 Meyi popita ku khoti.

Iwo anati nkhani ngati yobweretsa pamodzi mbali ziwiri zomwe zikukangana pamakhala zovuta zambiri koma ngati PAC iwo akugwiritsa mfundo za demokalase komanso zachilungamo zomwe pena sizikomera mbali ina.

“Zina mwa mfundo zomwe timatha kukamba zimatha kugwirizana ndi akumbali yotsutsa ndipo ambali ya boma amati tili mbali yotsutsa. Pena timatha kugwirizana ndi zomwe akunena ambali ya boma ndipo otsutsa aja amati tili mbali ya boma. Koma izi sizitifooketsa chifukwa ife taima pa zomwe ndi zabwino ku dziko lathu,” anatero Ambuye Msusa pouza AMECEA News Online.

Litakumana ndi mabungwe omwe siaboma komanso zipani zotsutsa boma, bungwe la PAC likukonza zokumanaso ndi Pulezidenti Mutharika pa nkhani yomweyi yobweretsa mtendere ndi bata ku m’dziko muno.