‘Kukhale kampeni yopanda ziwawa, dzavotereni atsogoleri akukhosi kwanu’
Wolemba: Joseph Kayira
Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lapempha anthu amene analembetsa pa chisankho chimene chinachitika pa 16 Seputembala chaka chatha kuti adzatuluke mwaunyinji ndi kukavotera atsogoleri a kumtima kwawo komanso kuti ku dera la Mulunguzi m’boma la Balaka kukhale kampeni yopanda ziwawa pa chisankho chapadera chomwe chichitike pa 30 Juni chaka chino.
Pokhazikitsa nthawi ya kampeni ya chisankho chapaderachi, kutsatira chigamulo cha khoti la apilo pa 28 Epulo chaka chino, makomishonala a MEC kudzanso akuluakulu ena omwe anali nawo pa msonkhanowo pa 1 Meyi pa Kankao Teachers Development Centre
ku Balaka, ati makandideti omwe anapikisana pa chisankho cha chaka chatha ndi omwe apikisanenso ulendo uno.

Kambulire: Sipakhala kalembera wina ayi (Chithunzi: Joseph Kayira)
Komishonala Phillip Kambulire anati chigamulo cha khoti la apilo chikutanthauza kuti chisankho cha aphungu cha chaka chatha mdera la Mulunguzi, chafufutidwa ndipo tsopano anthu a mderalo ali ndi mwai wosankhanso phungu watsopano. Pa chisankho cha chaka chatha, bungweli linalengeza kuti anapambana ndi a Ireen Mambala, woima paokha. Koma a James Makhumula, a chipani cha Democratic Progressive (DPP) anakamang’ala ku khoti ponena kuti panali zolakwika pa chisankhocho.
Ena amene anapikisana nawo pa chisankho cha phungu wa Nyumba ya Malamulo ndi a Jones Chamangwana, a chipani cha Malawi Congress (MCP); a Chikumbutso Harry Chanthunya, oima paokha; a Daniel Chikoti, a chipani cha UTM; a Laston Ronnex Makuluni, oima paokha; a Nanariwa Dick Nanguwo, a chipani cha Peoples Development Party (PDP); a Dorrah Eliya Samson, a chipani cha United Democratic Front (UDF); a Lucy Tchale, oima paokha; ndi a Frank Washon, oimanso paokha.
“Ndondomeko zina zokhuza chisankho chapaderachi zisinthapo. Mwa zina, ndi anthu okhawo amene anapikisana pa chisankho cha pa 16 Seputembala amene apikisanenso. Sipakhala zoti ena alowerereponso ayi. Palibenso kalembera watsopano; woyenera kuvota ndi wokhawo amene anavota pa 16 Seputembala aja,” anatero komishonala Kambulire.
Iwo anapempha anthu kuti ayambepo kutsimikizira maina awo ngati akupezeka mkaundula potsatira ndondomeko zimene zaikidwa. Mwa zina, anthu atha kufufuza ngati maina awo alimo mkandula pogwiritsa ntchito nambala ya lamya ya m’manja yomwe ndi *2509# ndipo izi zikutheka lamya ya m’manja ya mtundu uliwonse.
A Kambulire anati bungwe la MEC ligwirana manja ndi adindo osiyanasiyana – mabungwe, mipingo, makandideti a zipani komanso oima paokha, komanso mafumu mwa ena – kuti chisankho chiyende mwadongosolo, wopanda ziwawa, zolakwika ndi madandu.

Dr Fabiano: Tiyeni tigwirane manja pa ntchitoyi (Chithunzi: Joseph Kayira)
“Ndi cholinga chathu kuti anthu akwaniritse ufulu wawo wosankha atsogoleri amene akuwafuna popanda mavuto. Choncho tikufuna kugwiriana manja ndi atsogoleri onse mdera lino, komanso mu boma la Balaka, kuti chisankhochi chiyende mwa chilungamo ndi mtendere,” anatero komishonara Kambulire.
Komishonara Dr Emmanuel Fabiano, omwenso anali nawo pa mwambowo, anapempha anthu osiyanasiyana amene akutenga nawo gawo pa ntchito yoyendetsa chisankho chapaderachi, kuti agwire ntchito yawo mwaukadaulo ndi motsata malamulo.
“Tikufuna kupempha onse amene akutenga nawo gawo pa chisankhochi kuti agwire ntchito yawo mozipereka. Anthu a mderali afikiridwe ndi uthenga woyenera kuti azathe kuvota ndi kusankha atsogoleri a kumtima kwawo. Izi ziyenera kuchitika msanga chifukwa nthawi yatha.
“M’madera ena m’mene muli zisankho anthu anayamba kale kumva uthenga wa chisankho. Kuno zinthu zachitika mwadzidzidzi kaamba ka chigamulo cha khoti. Choncho tipemphe kuti adindo achite machawi pofikira anthu ndi uthenga wa chisankho kuti amene analembetsa aja azavote ndi kusankha atsogoleri amene akuwafuna,” Komishonara Dr Fabiano anatero.

Mdala: Tili ndi chiyembekezo kuti zonse ziyenda bwino (Chithunzi: Joseph Kayira)
Bwanamkubwa wa boma la Balaka, a Bibu Yusuf Mdala anati chigamulo cha khoti chipereka mwai kwa anthu a mderalo kuti asankhenso atsogoleri amene akuwafuna – ndipo potero deralo lidzakhala ndi mwai wa zitukuko zosiyanasiyana.
“Panali nkhawa kuti dera lino likhala lopanda phungu wa Nyumba ya Malamulo kwa kanthawi, koma pamene tsiku la chisankho laikidwa kale zikupereka chiyembekezo kuti posachedwapa anthuwa asankha phungu amene akumufuna. Zikatero ndiye kuti nawo apindula ndi thumba la ndalama la kudera la Constituency Development Fund (CDF) ndi zitukuko zina,” anatero a Mdala.
Iwo anati phungu wa Nyumba ya Malamulo ndi wofunikira m’magawo ambiri a chitukuko ku dera, kotero kuti pamene boma la Balaka likuika ndondomeko zake za chitukuko, ziwachitiranso ubwino anthu a mdera la Mulunguzi kukhala ndi phungu wawo kuti ayendere limodzi ndi madera ena onse m’bomalo.

Mfumu Chanthunya: Anthu asankhe mwanzeru (Chithunzi: Joseph Kayira)
Ndipo polankhulapo za kukonzedwanso kwa dongosolo loti kuderalo kukhalenso chisankho, Mfumu Chanthunya inati anthu a mdera la Mulunguzi tsopano ali ndi mwayi wosankha atsogoleri amene akuwafuna kuti awatumikire monga m’mene akufunira.
“M’mene chigamulo cha khoti chinabwerera muja kunali ngati taferedwa mdera lino; tikufuna tione kuti mlowam’malo [wa phungu wakale] akhala ndani. M’mene zakhaliramu, monga mafumu, tikhala tikuuza kuti kasankhidwe kakhale kabwino kwambiri; komanso kusankha mwanzeru, kuti mwina munthu amene tingamusankhe atithandize mdera lino,” Mfumu Chanthunya inatero.
