Abwenzi a chipatala cha Balaka ayendera wodwala
Wolemba: Joseph KAYIRA
Gulu la Friends of Balaka District Hospital pa tsiku la anakubala linakayendera odwala pa chipatalachi komwe linakayenderanso mbali yomwe moto unawononga khitchini, ndi maofesi.
Gululi lomwe linali loyamba kuthandizapo ndi zipangizo moto utangotentha chipatalachi linapereka chakudya, nsalu ndi katundu wina kwa odwala omwe anagonekedwa pa chipatalachi.
Bambo Piergiorgio Gamba, omwe anali m’modzi wa akuluakulu omwe anatsogolera gululi pomwe linakayendera odwala pa chipatalachi anati ubale wawo ndi chipatala cha Balaka ndi wakalekale ndipo kuyendera odwala inali njira imodzi yolimbikitsana kuti ndizotheka kuthandizana pa zimene anthu amasowa pa umoyo wawo.
Iwo amalankhula izi mogwirizana ndi zomwe gulu la Friends of Balaka District Hospitala anachita pothandiza kuti magetsi ndi madzi ayambenso kupezeka moto utatentha chipatalachi miyezi ingapo yapitayo.
“Umoyo wabwino ndi wa-thanzi ndi wofunikira kwambiri. Kubwera kwathu kudzawaye-ndera odwala pa tsiku la anakubala ndi chinthu cha tanthauzo kwa ife. Tinenenso kuti pa chipatala chino panachitika ngozi ya moto yomwe inawononga zinthu za-mbiri. Ife ndi abwenzi ena tathandizapo koma sikuti mavutowa atha ayi.
“Tiwapemphe anthu enanso akufuna kwabwino kuti abwere ndikuthandizapo chifukwa ma-vuto alipo ambiri. Ulendo wativumbulutsiranso zambiri zomwe zikufunika pachipatala chino. Tigwirane manja ndi anzathu a ntchito za umoyo ndi zachipatala kuti umoyo ubwerere mwakale komanso usinthike pachipatala chino pothandizapo pa mavuto omwe taonawa,” anatero Bambo Gamba.
Iwo analimbikitsanso umoyo wozidalira chifukwa anthu ali ndi kuthekera kokonzanso chipatala chawo potsatira chitsanzo chomwe awonetsa a Friends of Balaka District Hospital.
“Zinazi tikhoza kukwanitsa patokha. Tisamangolira kudikira kuti ena atithandize. Kuthandiza komwe ife tachita pa chipatalachi ndi chiyambi chabe. Enanso abwere ndithu ndikuona m’mene angathandizire.
“Uthenga wopita kwa anthu aku Balaka ndi woti chipatala chayambanso kugwira ntchito ndipo apite kukalandira chithandizo,” iwo anatero.
Mu uthenga wawo kwa anakubala, Bambo Gamba anapitiriza kunena kuti ndikofunika kuganizira ntchito imene amagwira madotolo, aphunzitsi ndi ena amagwira pogawa ndi kuteteza moyo.
“Awanso ndi anakubala wofunikira kwambiri. Tikuyenera kugwirana nawo manja pa ntchito yawo yofunikira kwambiri,” anatero Bambo Gamba.
A Patrick Bwanali omwe ndi wapampando wa Friends of Balaka District Hospital anati anachiona chamtengo wapatali kuka-yendera odwala pa tsiku la anakubala poganiziranso mavuto omwe chipatalachi chikukumana nawo chitikireni ngozi ya moto.
“Ife ngati a Friends of Balaka District Hospital takhala tikupempha anthu kuti tithandizepo pa ngozi yomwe inachitika ija. Anthu akufuna kwabwino anathandiza ndipo pano monga mukuonera chipatalachi chikugwira ntchito tsopano. Koma mavuto sikuti atheratu. Pali zambiri zomwe anthu angathandizepo,” anatero a Bwanali.
Iwo ati chofunikira kwambiri pa chipatalachi chinali kuonetsetsa kuti magetsi ndi madzi alipo “chifukwa popanda zimenezi chipatala sichingagwire ntchito bwino izi ndi zoyambirira ndipo ziyenera kukhalapo basi.”
Mkuluyu anati pokhala matenda sadikira munthu, kunali kofunika kuti a Friends of Balaka District Hospital alowererepo zinthu zinafike poipa kwambiri. A Bwanali anati ndi wothokozanso mwapadera chipatala cha Comfort Community chomwe ndi nthambi imodzi ya Andiamo Youth Cooperative Trust, posa-malira ena mwa odwala maka amayi oyembekezera pa nthawi yomwe chipatalachi chinaimitsa ntchito zake.
“Tiwayamikire a Comfort Community Hospital chifukwa cha ntchito yabwino yomwe agwira pa nyengo yovutayi. Nawo tsopano amasuka. Iwo ana-samalira kwambiri amayi oye-mbekezera ndi ena ndipo pa ichi tikuti zikomo,” anatero a Bwanali.
A MacArthur Makata, omwe ndi m’modzi wa akuluakulu a chipatala cha Balaka anati ndiwothokoza kuti gululi linaganiza zodzawayendera odwala awo pa chipatalachi.
“Ndife wokondwa kuti odwala alandira chakudya komanso mphatso zina pa tsiku la anakubala ngati lero.
Ndi mavuto amene takumana nawo patokha sitikanakwanitsa kuchita zinthu za mtengo wapatali zomwe zachitika lerozi,” anatero a Makata.
Iwo anati mpaka pano malo ochapira, khitchini ndi kwina komwe kunakhuzidwa ndi moto sikunakonzedwebe moti chakudya amakonzera pamtetete.
“A Friends of Balaka anatigulira makina ochapira koma timangowagwiritsa ku theatre chifukwa ndi kumene kuli kofunikira kwambiri. Kwinako timachita kutumiza zinthu ku zipatala zina za boma kuti atithandize. Choncho mavuto adakalipobe pa chipatala chino.,” anatero a Makata.
Iwo ati zitenga nthawi kuti chipatalachi chifike pogwira bwinobwino ntchito yake ngati kale chifukwa pali zambiri zomwe zikuyenera kukonzedwanso. A Makata ali ndi chikhulupiriro kuti boma ndi anthu akufuna kwabwino achita chotheka kuti zonse zibwerere mchimake.