General

‘Adindo tengani nawo mbali pofalitsa uthenga wa TB ndi khate’

By Rose Chipumphula Chalira

Unduna wa za Umoyo kudzera mu nthambi yake yoona za matenda a chifuwa cha TB ndi khate, wapempha atsogoleri andale, mabungwe ndi anthu ena onse kuti atenge nawo mbali pofalitsa uthenga wa zizindikiro za chifuwa chachikulu. 

Undunawu wanena izi  kudzera m’chikalata chomwe mlembi waku Unduna waza umoyo, a Samson Mdolo asayinira ndi kuchitulutsa. Mutu wa mwambo wa chaka chino ndi Zowonadi Tikhoza Kuthetsa TB, Tiyigonjetse TB kuti matendawa akhale mbiri yakale.’

Chiponda: Akakhala mlendo wolemekezeka (Chithunzi: Mana)

Chikalatachi chikudziwitsanso anthu m’dziko muno kuti mwambo wokumbukira matenda a chifuwa chachikulu ndi khate umene umachitika pa 24 Marichi chaka chilichonse, ulendo uno udzachitikira pa bwalo la masewero la sukulu ya Khaya, kwa Mfumu yayikulu Chikumbu m’boma la Mulanje. 

Malingana ndi chikalatachi, pali mphekesera zabodza zosiyanasiyana ndiponso kusalana pakati pa anthu pa nkhani zokhudzana ndi matenda a TB ndi khate chifukwa choti anthu sakupeza mauthenga oyenerera. 

Mwazina, chikalatachi chati kafukufuku amene adachitika m’dziko muno m’chaka cha 2014 adasonyeza kuti pa anthu 100,000 alionse, anthu 334 anali ndi chifuwa cha TB. 

Kafukufukuyu adasonyezanso kuti abambo ambiri ndi amene akudwala nthendayi kusiyana ndi amayi, komanso chiwerengero cha anthu odwala chifuwachi ndi chokwera kwambiri m’mtauni kusiyana ndi m’midzi.

Chikalatachi chati dziko lino likuchita chotheka pofuna kuthana ndi matendawa mothandizana ndi mabungwe akunja omwe akutenga nawo mbali polimbana ndi kufala kwa matendawa. 

Malingana ndi mkulu woona matendawa ndi kumemeza anthu ku nthambiyi mayi Beatrice Mtotha Nindi, pa mwambo wa chaka chino mlendo wolemekezeka ndi Nduna yowona ntchito za umoyo, a Khumbize Kandodo Chiponda.

Kumwa mankhwala motsatira malamulo kumathandiza wodwala kuchira msanga (Chithunzi: Internet)

A Nindi anati matenda a chifuwa chachikulu cha TB ndi khate ndiochizika ngati odwala omwe apezeka ndi matendawa akutsatira upangili wa zaumoyo. 

A Nindi anayamikira ubale wabwino omwe ulipo pakati pa nthambi yowona matendawa ndi atolankhani omwe amawonetsa chidwi cholemba nkhani mwa ukadaulo. Izi zimachititsa nthambiyi kupereka mphatso kwa atolankhani omwe achita bwino pa ntchito yawo ngati njira imodzi yowalimbikitsa kuti asafooke pogwira ntchitoyi.

Iwo anati boma, mabungwe omwe siaboma ndi ena akugwirana panja polimbana ndi kufala kwa matendawa chifukwa ndi ochizika ngati wodwala wawona zizindikiro msanga ndikupita ku chipatala mwachangu. “Komanso wodwala ayenera kumwa mankhwala mwandondomeko osati kuchita ukamberembere ndi zina zomwe zimachititsa odwala kusachira msanga,” a Nindi anatero.