‘Admarc ilibe ndalama zogulira mbewu

Wolemba: Bartholomew Boaz

Ngakhale ndi zowawa kuzimva koma ndi chilungamo chake kuti bungwe logula ndi kugulitsa mbewu m’dziko muno la Admarc lilibe ndalama zogulira mbewu munthawi yokolola.

Mkulu wa bungweli a Felix Jumbe ndiye waulula pamene amakaonekera pamaso pa komiti ya aphungu aku Nyumba ya Malamulo yoona zaulimi.

Chaka ndi chaka bungwe la Admarc limayamba kugula mbewu mochedwa alimi atagulitsa kale kwa anthu abizinezi. Nthawi zambiri Admarc imadikira kuti Nyumba ya Malamulo ikambirane ndondomeko ya chuma mu Julaye momwe mumakhala ndalama za bungweli zogulira mbewuzi.

Nchifukwa chake limayamba kugula mbewu mu Julaye pena Ogasiti.

A Jumbe ati ndi chifukwa chake bungweli likufuna litabwereka ndalama yokwana K300 biliyoni yoti itha-ndizirenso kubwezeretsa Admarc m’chimake kuti idzitha kugula mbewu munthawi yake.

Iwo ati ndalamayi ithandizanso kuti misika ya Admarc ifalikire kumadera ambiri am’dziko muno monga zinkachitikira kale.

“Ndalama imeneyi ithandiza kuti Admarc idzigwira ntchito zake uku ikupanga phindu ndipo zimenezo zipangitsa kuti tizigula mbewu zambiri kwa alimi,” anatero a Jumbe, omwe anati ngongoleyi ikhale yobwenzedwa kwa zaka khumi.

Jumbe: Mkulu wa Admarc

Iwo anati Admarc ikusowa ndalama yokwana pakati pa K220 biliyoni mpaka K230 biliyoni kuti idzikwanitsa kugula mbewu zonse za alimi chaka chilichonse.

Wachiwiri kwa wapampando wa komiti ya aphungu yoona zaulimi a Ulemu Chilapondwa anati Admarc itakwaniritsa zomwe akonzazo ndiye kuti alimi sangamaberedwe ndi anthu abizinezi ngati mmene zikuchitikira pano.

“Tikunena pano alimi ang’onoang’ono akuberedwa mitengo ndi abizinezi chifukwa palibe bungwe limene likumaika mitengo yogulira mbewu,” anatero a Chilapondwa.

Iwo anati ayesetsa kupempha boma kuti liganizire kuthandiza Admarc kupeza ngongole imeneyi kuti zinthu ziyambenso kuyenda bwino.