GeneralNkhani Zina

Amalawi, mabungwe akuti a Mutharika abweretsa chiyembekezo kudzera mu SONA

Wolemba: Faith Kaisi MATHOTHO

Magulu ambiri, atsogoleri a mabungwe komanso amipingo kudzanso andale, ayamikira mfundo zomwe zili mu ndondomeko ya m’mene zinthu zilili m’dziko muno (State of the Nation Address – SONA) yomwe Pulezidenti Peter Mutharika anaitulutsa mu Nyumba ya Malamulo masiku apitawa mu mzinda wa Lilongwe.

Omwe aperekapo kale ndemanga zawo pa SONA ati ndondomekoyi ikupereka chiyembekezo kwa Amalawi – maka pa nthawi ino pamene boma la a Mutharika liri pa kalikiliki wofunanso kukonza chuma cha Malawi, pomwe pakali pano sichili bwino.

Mkulu wa bungwe la Centre for Youth Empowerment and Civic Education (CYECE), a Lucky Mbewe, ati masomphenya omwe a Mutharika ali nawo ali ndikuthekera kotukula dziko lino, chomwecho adindo komanso nzika za dziko lino, zikuyenera kutengapo mbali kuti Malawi afike pa dziko la mkaka ndi uchi.

“Ife ngati amene timamenyera ufulu wa achinyamata ndi ana ndife okodwa ndi thumba la ndalama za ngongole lomwe mtsogoleri wa dziko lino wakhazikitsa pofuna kupereka mwai wa ntchito kwa achinyamata omwe ali mmavuto akusowa kwa ntchito. Kuphatikiza apo, ndifenso okondwa ndi kutsegulidwa kwa sukulu za luso la manja, zomwe zipereke danga kwa achinyamata omwe ali m’midzi kuti aphunzire maluso osiyanasiyana,” anatero a Mbewe.

Mutharika: Boma langa likufuna kusintha zinthu kuti zifike pabwino (Chithunzi: Internet)

A Mbewe anapitiriza kunena kuti mfundo ya ntchito za migodi, maphunziro komanso ulimi zikupereka chiyembekezo chopititsa patsogolo chitukuko cha dziko la Malawi. Iwo anapitiriza kulangiza boma kuti likhwimitse chitetezo pa nkhani yothana ndi ziphuphu ndi katangale ndicholinga choti kayendetsedwe ka chuma cha dziko lino kasinthe.

“Chuma cha dziko lino chakhala chikusokonekera kaamba ka ulamuliro womwe unalibe luso ndi ukadaulo lakutsogolera. Ichi nchifukwa chake chuma chakhala chikuonongeka mu nthawi yomwe chikanakhodza kusintha miyoyo ya Amalawi pogwira ntchito za chitukuko cha dziko lino,” anatero a Mbewe.

Pothirirapo ndemanga pa nkhaniyi, bungwe la achinyamata la Youth for Action Campaign (YAC), nalo layamikiranso a Mutharika kudzera mu chikalata chomwe chinasainidwa ndi mkulu wa bungweli, a Jackson Caesar Msiska. Iwo apempha mabungwe oyima paokha komaso magulu ena okhuzidwa kuti agwirane manja ndi boma ndicholinga choti masophenyawa  apindulire Amalawi.

Chikalatachi chinati ndikofunika kuti pakhazikitsidwe ndondomeko zoyenera zoti pasakhale   sankho kapena katangale ikafika nthawi yoti achinyamata komanso amayi atenge ngongolezi.

Chikalata chomwe linalemba bungwe la YAC

“Ngati bungwe ndife okodwa ndi ndondomeko zomwe mtsogoleri wa dziko linoyu waika, makamaka mfundo zopereka danga kwa achinyamata komaso a mayi,” chatero chikalatacho.

Magulu achipembezo nawo ayamikira a Mutharika potsindika kuti mfundo zawo zili ndi kuthekera kobwedzeretsa chuma cha dziko lino m’chimake.

Izi ndi malingana ndi zomwe M’busa wa mpingo wa Enlighted Christian Gathering (ECG), Prophet Shepard Bushiri analemba pa tsamba lake la mchezo la Facebook.

Prophet Bushiri: Pakufunika njira zabwino ndi zokhazikika (Chithunzi: Internet)

“Kuti zonsezi zitheke pakufunika kukhazikitsa njira zokhazikika, za chilungamo komanso utsogoleri womvera anthu, ndicholinga choti dziko lino lipite patsogolo,” anatero mukulemba kwawo a Bushiri.

Pamene amatsegulira zokambirana za aphungu a Nyumba ya Malamulo zokhuza ndondomeko ya chuma cha boma (bajeti), mwa zina, a Mutharika ananenetsa kuti athana ndi aliyense amene apezeke kuti akuchita katangale. Iwo ati ndi cholinga chawo kukonza chuma cha boma kuti Amalawi asapitirire kufinyika, monga m’mene zinthu zilili panomu.