Amayi ali ndi malo abwino ochirira pa chipatala cha Kwitanda
Wolemba: Joseph Kayira
Palibenso chifukwa choti amayi azikaberekera kwa azamba kapenanso patchier kaamba koti anthu ozungulira chipatala chaching’ono cha Kwitanda, mdera la Mfumu Nsamala m’boma la Balaka akusimba lokoma chifukwa pa chipatalachi patsegulidwa chipinda chamakono chomwe amayi oyembekezera akuchilirako.
A Chiponda kudula riboni potsegulira chipinda chochirira amayi (Chithunzi: Joseph Kayira)
Nduna ya Zaumoyo a Khumbize Kandondo Chiponda ndiyo yatsegulira chipindachi Lolemba pa 20 Januwale ndipo iyo yalimbikitsa amayi kuti azipita kuchipatalachi chifukwa kuli akadaulo amene angawathandize akakhala kuti ndioyembekezera.
“Chipinda chomwe chatsegulidwa pa chipatala cha Kwitanda ndi chapamwamba kwambiri. Muli zipangizo zamakono ndipo amayi akuthandizidwa mwaukadaulo. Boma la Malawi likufuna zipatala zonse – kaya ndi kumudzi kaya ndi kutauni – zikhale ndi zipangizo zamakono kuti anthu azithandizidwa bwino. Tikufuna zipatala zazing’ononso zizikhala ndi zipangizo monga zomwe taona pa chipatala cha Kwitanda,” anatero a Chiponda.
Iwo ati kumangidwa kwa chipinda chochilira amayi pa chipatala cha Kwitanda, zachitika mogwirizana ndi mfundo za mu ndondomeko ya chitukuko ya Malawi 2063, kaamba koti ndi anthu a umoyo wathanzi omwe angathandize pa ntchito yotukula dziko lawo.
A Chiponda afotokozanso kuti chipindachi chisanamangidwe amayi amayensa mtunda wautali kupita ku zipatala zomwe kuli zipinda zochilirako monga ku boma komanso ku Utale. Koma kumangidwa kwa chipindachi kwachepetsa ululu umene amayi amamva akamayenda kupita kuchipatala.
Nyumba yatsopano momwe amayi akuchirira yomwe yamangidwa pa chipatala cha Kwitanda (Chithunzi: Joseph Kayira)
“Boma la Pulezidenti Lazarus Chakwera lakangalika kumanga zipatala komanso malo ochilira monga apa Kwitanda chifukwa akufuna amayi asamayende mitunda italiitali akamakachira. Tikuchita izi m’maboma onse ndi cholinga choti pasakhale boma lotsalira. Tikuyesetsanso kuti tilembe antchito okwanira mzipatala kuti amayi komanso wina aliyense amene akufuna thandizo la zaumoyo asamavutike,” atero a Chiponda.
Ndondomeko ya bungwe la maiko onse la United Nations la Sustainable Development Goals ya chitatu imalimbikitsa umoyo wabwino kwa onse kuphatikizapo amayi. Cholinga cha mfundoyi nkuti pomafika mchaka cha 2030 lidzakhale litachepetsa chiwerengero cha amayi amene amamwalira kaamba ka uchembere.
Amayi amene amakhala m’madera akumidzi, kutali ndi zipatala ndi amene amamwalira kapena kukhuzidwa kwambiri ndi imfa kapenanso mavuto omwe amadza kaamba ka nkhani za uchembere.
Phungu wadera la Kumwera kwa Balaka, a Ireen Mambala anati ndiwokondwa kuti pa chipatala cha Kwitanda tsopano pali chipinda chochilira amayi. Iye wafotokozanso kuti m’mbuyomu amayi amayenda mtunda wautali kuti akachire.
“Kambirimbiri ndapezapo amayi ali panjira zitasokonekera. Ndawatengapo pa galimoto yanga kukawasiya kuchipatala. Ambiri kuno ankapita ku Utale komwe kuli kutali kwambiri. Koma ndikumangidwa kwa chipinda chatsopanochi pa Kwitanda zinthu zakhala bwino. Amayi azithandizidwa pafupi,” anatero a Mambala.
Ena mwa akuluakulu kusirira mphatso mchipindacho (Chithunzi: Joseph Kayira)
A Mambala apemphanso unduna wa Zaumoyo kuti uthandizenso kumanga malo a odikirira odwala mzipatala zazing’ono kuti amayi oyembekezera azibwera kuchipatala ndi owadikirira.
“Amayi ambiri amabwera mochedwa ku chipatala kuti azachire chifukwa palibe malo amene owadikirira angakhale. Choncho titamanga nyumba zodikirira zambiri zizathandiza kuchepetsa mavuto omwe angabwere kaamba kakuchedwa kufika ku chipatala,” anatero a Mambala.
Chipindachi achimanga ndi ndalama zochokera kuthumba la District Development Fund (DDF) zosachepera K49 miliyoni.