General

‘Ana abwerere ku sukulu’

Wolemba: Joseph Kayira

Gawo 23 la malamulo a dziko lino (Konstichushoni) likunenetsa za kufunika koteteza ana ku m’chitidwe uliwonse womwe ungaike moyo wawo pachiswe, kusokoneza maphunziro awo komanso kubweretsa chisokonezo pa umunthu wawo powasokoneza ubongo, kaganizidwe ndi momwe angatukulire miyoyo yawo. Lamuloli likupitiriza kunena kuti mwana ndi munthu yemwe zaka zake zikulekeza 16.

Koma kwa nthawi yaitali ana m’dziko muno akhala akuchitiridwa nkhanza zosiyanasiyana kuphatikizapo kuwasokonezera maphunziro awo. Makolo ambiri amatha kutuma mwana wawo kuti akagulitse malonda monga mandazi ndi zina zotero pomuuza kuti asapite ku sukulu. Uku ndikuphwanya Gawo 23 la malamulo a dziko lino ndipo uwu ndi mlandu ndithu.

Kayuni: Amene anakumana ndi ngozi monga ya namondwe wa Freddy tiwathandize (Chithunzi: MML)

Kulekerera mwana kuti azipanga zimene iye akufuna m’malo mopita ku sukulu ndi mlandunso kaamba koti kholo liri ndi udindo wolera mwana motsata malamulo a dziko lino. Chimodzimodzinso ana amene anakhudzidwa ndi ngozi ya namondwe wa Freddy yemwe anaononga kwambiri zinthu ndi miyoyo ya anthu maka m’maboma a kum’mwera kwa dziko lino, akuyenera kutetezedwa ndi kupatsidwa mpata wobwereranso ku sukulu.

Sipokhapo. Asungwana omwe anakhuzidwa ndi namondweyu ndi mavuto ena omwe amapsinja asungwana, kufika poganiza zosiyira maphunziro panjira, nawo akuyenera kulimbikitsidwa ndi kubwerera ku sukulu.

Pofuna kuthandiza kuchepetsa penanso kuthetsa kumene mazunzo komanso zokhoma zomwe achinyamata – maka asungwana – amakumana nazo pomwe akusakasaka mwai wamphunziro, bungwe la Centre for Alternatives for Victimised Women and Children (CAVWOC) ndi la Oxfam, agwirana manja kudzera mu pulojekiti yomwe ikupereka uphungu kwa atsikana ndi ana omwe ali pa chiopsezo yomwe pachingerezi akuitchula kuti Psychosocial Counselling to Girls and other Vulnerable Children.

TA Phalula akuti anthu agwiritse mwai wachitukukochi mwanzeru (Chithunzi: MML)

Mwa zina pulojekitiyi ikuunika nkhanza zomwe zimakhalapo pakati pa amuna ndi akazi maka m’madera omwe anakhuzidwa ndi namondwe wa Freddy – kuphatikizapo kwa Phalula, m’boma la Balaka. Pulojekitiyi ikuthandizapo popereka upangiri kwa anthu ogwira ntchito za chitetezo cha m’dziko (apolisi), aphunzitsi, akuunduna woona kuti palibe kusiyana pakati pa amayi ndi abambo (gender and social welfare) komanso kuonetsetsa kuti achinyamata akulandira thandizo loyenerera la zaumoyo.

Tiyambe kuchitapo kanthu

A Twambirire Kayuni, omwe ndi mkulu woona zamaphunziro ndi kusasiyana pakati pa amayi ndi abambo ku bungwe la Oxfam akuti ana omwe anakumana ndi ngozi ya namondwe wa Freddy kudzanso ngozi zina zachilengedwe, akuyenera kulimbikitsidwa kuti abwerere ku sukulu.

Iwo akuti anawa akaganizira za mavuto omwe anakumana nawo kumakhala kovuta kuiwala ndipo nkofunika kuti azithandizidwa ndi anthu omwe angawathandize kuti abwererenso mwa kale monga ana ena onse.

“Ngozi imene ija inapangitsa kuti anthu ataye miyoyo, katundu wawo ndi zina zambiri. Kudutsa mnyengo zimene zija kunasokoneza miyoyo ya anthu. Ana ena anataya makolo awo ndipo panali nkhawa yoti maphunziro adzapitiriza motani. Pulojetikiyi imene ili kwa Phalula ndi madera ozungulira ikuthandiza kuchepetsa ululu umene anthuwa akhala akudutsamo,” akutero a Kayuni.

Chakwera: Pulojekitiyi ndiyothandiza kwambiri (Chithunzi: MML)

Iwo akuti ana ena anafika potaya chikhulupiriro ndipo amaona ngati ngoziyo anali mathero a zonse. Koma a Kayuni akuti pulojekitiyi yabweretsa chilimbikitso pakati pa achinyamata, maka asungwana omwe tsopano abwereranso ku sukulu. Kwa amene amakhala kutali ndi sukulu anapatsidwa njinga zomwe amakwera kuti azifika mu nthawi yake kusukuluko.

“Palinso ana ena amene mwina amatha kusalidwa kaamba ka zomwe anadutsamo ndipo safunanso kubwerera ku sukulu. Ena amakhala ndi mantha kulankhula chifukwa sadziwa kuti akalankhula akumana ndi zotani. Pulojekitiyi ikuthetsa zonsezi kuti aliyense akhale ndi mwayi wamaphunziro.

“Komanso tikulimbikitsa kuti ana azitha kulankhula ndi kuulula za nkhanza zomwe amakumana nazo. Ichi nchifukwa chake taphunzitsa akuluakulu a ntchito zosiyanasiyana monga aku polisi, aphunzitsi ndi antchito zina za boma kuti pa momwe angathandizire ana omwe adutsa mu zokhomawa,” akutero a Kayuni.

A Kayuni akulangizanso makolo amene ali ndi mchitidwe wotumiza ana ku malonda kuti izi ndi zosemphana ndi malamulo a dziko lino komanso malamulo amene anakhazikitsidwa m’madera.

‘Tisalekerere m’chitidwewu’

Mfumu Phalula ikuti siikufuna kuti anthu a m’dera lake alekerere m’chitidwe wotumiza ana kumalonda pamene anzawo ali m’kalasi. Iyo yati makolo amene akuchita m’chitidwewu ayenera kulandira chilango.

Khuoge: Sitisekerera ana amene azithawa kusukulu (Chithunzi: MML)

“Tagwirizana ndi mafumu ena onse kuti kuno kwa Phalula sitilolanso kholo kumatumiza ana kumalonda pamene ana akuyenera kulandira maphunziro. Kubwera kwa Oxfam ndi CAVWOC kwasintha zinthu kwambiri mdera langa lino. Choncho sitikufuna chitukuko choterechi chipite pachabe.

“Ana ena amakalowa m’mavidiyo show pamene anzawo ali m’kalasi. Ndikufuna makolo limene mwana wake wapezeka koonera vidiyo pamene ana ena akuphunzira, makolowo akuyenera kulandira chilango. Tiyeni titeteze anawa. Tiyeni tionetsetse kuti anawa akulandira maphunziro. Ndife amwayi kuti a Oxfam ndi CAVWOC anadzatipatsa chitukuko chimenechi. Akulipira fizi ya ana athu; akupereka njinga kuti akutali azitha kufika ku sukulu msanga. Anzathu ena alibe mwayi ngati wathuwu,” ikutero Mfumu Phalula.

Mfumuyi yati igwirana manja ndi apolisi kuti m’chitidwe wojombetsa ana ku sukulu uthe. Iyo yati ana amene sangapeze maphunziro lero alibe mwai mtsogolo muno ndipo adzakhala olephera pa moyo wawo.

Chauluka: Tili mkati mokhazikitsa malamulo (Chithunzi: MML)

Wamkulu wa apolisi pa polisi ya Phalula a Patrick Khuoge ati akugwirizana kwathunthu ndi zolinga za pulojekitiyi ndipo awonetsetsa kuti maphunziro sakusokonekera chifukwa mabizinesi komanso makolo amene sakufuna kutengapo mbali pa maphunziro a ana awo.

“Ana amene apitilize kuthawa kapena kujomba ku sukulu tikawapeza kumsewuku akuwonera mavidiyo tiwamanga. Tikawapeza akuchita malonda anzawo ali kusukulu tidzawatsekera. Ana akuyenera kukhala ku sukulu osati kumsika kapena ku msewu kumagulitsa malonda,” akutero a Khuoge.

Wapampando wa Phalula GVB Network, a Harris Chauluka, ati ndizoona kuti ana mderalo akukumana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo kuchitiridwa nkhanza. Iwo ati pakali pano malamulo akukonzedwa omwe agwire ntchito pa amene akuchitira ana nkhanza.

“Kwatsala apa ndi kuti aku ofesi ya bwanamkubwa akadindepo chidindo kuti tiyambe kuwagwiritsa ntchito. Malamulowa adzagwira ntchito pa makolo komanso anthu amene apezeke kuti akuchitira ana nkhanza zosiyanasiyana.

Ena mwa ophunzira amene anachita bwino kulandira mphoto zawo (Chithunzi: MML)

“Tikufunanso kuti apolisi akagwira ana amene akuchita malonda kapena apezeka akuonera mavidiyo, ayenera kulandira chilango. Ife tikugwirizana ndi a Oxfam ndi CAVWOC kuti ana asamachitiridwe nkhanza; akuyenera kupeza maphunziro kuti adzakhale pabwino. Malamulowa akayamba kugwira ntchito sitisekerera zolakwika. Komanso tikufuna makolo asamakalimbane ndi apolisi akagwira anawa,” akutero a Chauluka.

A Baxter Chakwera m’modzi wa akuluakulu aku khonsolo ya Balaka akupempha ana kuti asakopeke ndi zinthu zomwe zingasokoneze maphunziro awo koma kuti aike mtima pamaphunziro awo.

“Tiwapemphe ophunzira kuti achitenge ngati chinthu cha mwai kuti Oxfam ndi CAVWOC akuwathandiza. Ichi ndi chinthu cha mtengo wapatali. M’madera ena akulakalaka akanakhala ndi pulojekiti ngati imeneyi.

“Chofunika apa ndi choti makolo komanso amene amawayang’anira ana amene akupeza thandizo la zipangizo zosiyanasiyana kuti ayambepo kuwatsata anawa. Adziona malipoti awo teremu ikatha. Mwai ngati umenewu uzipita kwa okhawo amene ali ndi chidwi pa maphunziro. Ndiwapemphe mwapadera atsikana kuti asachite chibwana koma alimbikire kuti zawo ziyende,” akutero a Chakwera.

M’modzi mwa ophunzira, Takondwa, yemwe akuti akufuna kudzakhala pulezidenti (Chithunzi: MML)

Iwo akuti nkhanza ndi chinthu chimodzi chimene chimabweretsa chisokonezo pamaphunziro ndipo anthu akuyenera kugwirizana kuti izi zithe. Mkuluyu wati ana ambiri amene amachitiridwa nkhanza amajomba ku sukulu zomwe zimabwezeretsa maphunziro awo pambuyo.

“Tiwayamikire a Oxfam ndi ena onse omwe akugwira nawo ntchito mu pulojekitiyi chifukwa akubweretsa chiyembekezo pa maphunziro maka kwa ana amene amaona ngati zawo zinada. Awa ndi ana monga amene anakumana ndi namondwe wa Freddy uja. Koma kubwera kwa mabungwewa kwathandiza anawa kuti awonenso kuwala. Anawa alibenso chonamizira chifukwa ili ndi thandizo lopezekeratu,” akutero a Chakwera.

Mvetsetsani zamalamulo

M’modzi wa akuluakulu a polisi ya Balaka a Robert Njalammano, omwe amathandizira kwambiri pa nkhani za chitetezo cha kumudzi, ati anthu akuyenera kumvetsetsa zomwe malamulo akunena pa nkhani ya nkhanza kwa ana. Iwo atsindika kuti nkhanza za mtundu wina uliwonse pa ana ndizoletsedwa.

Iwo achenjeza kuti aliyense amene angachite ukwati ndi msungwana yemwe zaka zake sizinafike 16 adzamangidwa. Mkuluyu wati anthu akhale ndi chidwi pa nkhani za ana ndi zomwe malamulo akunena.

A Oxfam ndi CAVWOC akuti mtsikana wamakono apite ku sukulu (Chithunzi: MML)

“Ambiri amachita zinthu m’chimbulimbuli koma lamulo lidzagwira ntchito pa aliyense yemwe wachita ukwati kapena kugona ndi mwana yemwe zaka zake sizinapyole 16. Amene amavomereza maukwati wotere nawo adziwe kuti akuphwanya malamulo,” akutero a Njalammano.

Iwo ati ofesi yawo yayendera kale sukulu zambiri pofuna kudziwitsa anthu zamaufulu a ana komanso zomwe malamulo akunena pa nkhani za nkhanza. Pa maulendo ngati awa iwo akulimbikitsanso achinyamata zakufunika kolimbikira maphunziro mogwirizana ndi ndondomeko zomwe a Oxfam ndi CAVWOC akukhazikitsa kudzera mu pulojekiti yawo m’dera la Phalula.

Koma apolisiwa sakuyendera madera a kwa Phalula kokha koma boma lonse la Balaka poonetsetsa kuti nkhanza sidzikuchitika kwa ana ndi atsikana komanso kuwalimbikitsa kuti akhale omasuka poulula nkhanza zonse zimene amakumana nazo.

Memory Makiyi, yemwe ndi mmodzi wa apolisi omwe anaphunzitsidwa bwino m’mene angathandizire ana amene amakumana ndi nkhanza – maka m’madera ozungulira Phalula – wati ndizosangalatsa kuti anthu ambiri tsopano akubwera poyera kudzaulula za nkhanza zomwe amakumana nazo kuphatikizapo ophunzira mu sukulu za pulaimale ndi sekondale.

Makiyi limodzi ndi mwana yemwe amafuna atakhala wapolisi, kuonetsa setifiketi yake (Chithunzi: MML)

“A Oxfam ndi CAVWOC anationjezera maluso amene tikutha kugwiritsa ntchito pozindikiritsa anthu maka achinyamata za nkhanza. Pano nkhanza zikuchepa chifukwa anthu ayamba kudziwa zomwe malamulo akunena.

“Zimadandaulitsa ndi zoti munthu akagwirira mwana kapena kugona ndi wachichepere mabanja ena amabisa nkhanizi. Koma tikuwalimbikitsa kuti azibwera poyera ndi kudzapereka malipotiwa ku polisi,” akutero a Makiyi. Pali chikhulupiriro choti zolinga ndi khumbo la Oxfam ndi CAVWOC zikwaniritsidwa ndipo kuti asungwana ambiri achita bwino pa maphunziro atazindikira kuti mwayi umene apatsidwa ndiwamtengo wapatali. Chimodzimodzinso nkhanza zayamba kuchepa pakati pa achinyamata ndi asungwana kaamba koti ali ndi mwayi wokanena kumalo oyenerera kuti woganiziridwawo akumane ndi lamulo. Pamathero pa pulojekitiyi pali chiyembekezo choti dera la Phalula lidzasimba lokoma.