General

Anthu amawamvera atsogoleri amipingo – NCA/DCA

Wolemba: Rose Chipumphula Chalira

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a Norwegian Church Aid ndi Dan ChurchAid ( NCA/DCA), a Stefan Jansen ati atsogoleri a mipingo ali ndi kuthekera kofalitsa uthenga wokhudza kuchepetsa mimba za atsikana achichepere. 

A Jansen anayankhula izi m’boma la Machinga pa mwambo wokhazikitsa pulojekiti yokhudza za umoyo ndi maufulu ogonana ndi ubereki yoyendetsedwa ndi a chipembedzo.

Iwo anati pulojekitiyi, yomwe igwiridwe kwa zaka zitatu, ithandiza amipingo kutenga nawo mbali pofalitsa nkhani za uchembere wabwino kwa achinyamata – maka atsikana ndi kudziwanso zamaufulu awo. 

Wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo a Halima Daud anati boma likufuna kuthana ndi mimba za atsikana achichepere kuchoka pa 29 peresenti kufika pa 15 peresenti m’chaka cha 2030. 

Jansen: Pulojekitiyi ndiyofunika kwambiri (Chithunzi: Montfort Media)

Iwo anati atsikana akatenga mimba ali achichepere zimapereka chiopsezo pa ntchito za umoyo komanso umoyo wawo monga matenda a Fistula ndi zina zomwe zimabweretsa m’mbuyo ntchito za umoyo. 

“Mwana wa mkazi akatenga mimba asanakhwime zotsamwitsa pamoyo wake ndi zambiri komanso amasiyira sukulu panjira kumasamala mwana wobadwayo,” anatero a Daud.

Ndunayi inapempha makolo kuti asathamangitsire mwana wa mkazi ku banja kapena kutenga mimba ali wachichepere koma kumulimbikitsa maphunziro kuti azakhale nzika yodalirika.

“Mwandiona ine ndikanapanda kuphunzira, kapena kutenga mimba ndili wachichepere, sindikanakhala nduna komanso phungu. Makolo tiyeni tiwateteze ana pogwirana manja ndi amipingo onse pofalitsa uthengawu,” anatero a Daud 

Kazembe wa dziko la Norway kuno ku Malawi, a Ingrid Marie Mikelsen, ati kusintha kaganizidwe ndi kugwirana manja kwa boma, mabungwe omwe siaboma ndi ena kuthandiza dziko lino kuthana ndi mimba za atsikana achichepere. Iwo ati ntchitoyi siyosiyira boma lokha kapena amabungwe ayi. 

“Atsikana ambiri m’dziko lomwe ine ndikuchokera anakwanitsa maloto awo; chomwechonso atsikana kuno ku Malawi atha kukwaniritsa maloto awo ngati sakutenga mimba ali achichepere ndikupewa m’chitidwe wogonana asanakhwime,” anatero a Mikelsen.

Mgwirizano wa mabungwe wa NCA/DCA wayika ndalama zokwana K1.5 biliyoni zomwe agwilire ntchitoyi m’maboma a Nsanje, Chikwawa ndi Machinga kwa zaka zitatu.