Asirikali afa zipolopolo zili mkhosi
Anabwera atakonzeka, zida zonse zili potelopo, koma zidazi sizidali zokwanira kuthandizira asirikali aku Zomba kupambana nkhondo.
Ndithudi timu ya Red Lions yadzipatsa chi ntchito pa ulendo wake wofuna kubwerera mu Ligi yayikulu ya Super League pomwe yawomberedwa ndi chipolopolo chimodzi kwa zii ndi ana a Ekhaya aku Blantyre pa bwalo la Balaka lero masana.
Mmene zateromu, asirikaliwa tsopano Ali ndi mapointi 15 pomwe Ekhaya ili neng’a pamwamba ndi mapointi 19, onsewa kuchokera ku masewero 8.
Mu nkhondo yalero, asirikali abayidwa muvi nkhondo yothaitha mu mphindi zowonjezera 91, apa nkuti komanda wamkulu amaona mayendedwe a nkhondoyi atawonjezera mphindi zisanu ndi ziwiri kuti mwamuna awoneke.
Wolemba Precious Msosa
Zithunzi zikuonetsa osewera ena mwa osewera a Reds (avala zofiira) asakukhulupilira kuti abayidwa, kwinaku ndi ana a Ekhaya kusangalala atagwetsa Yericho. Zithunzi Precious Msosa