‘Atolankhani khalani ndi chidwi pa makontilakiti’
Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA
Atolankhani awapempha kuti akhale ndi chidwi pa nkhani yokhudza kugula katundu ndi kuchita zinthu poyera (Public Procurement Process) ndicholinga choti adzitha kutsata bwino za makontilakiti omwe amachitika.
Izi zinakambidwa pa maphunziro omwe bungwe la Hivos linachititsa mu mzinda wa Blantyre osula atolankhani pa nkhani yofufuza mwakuya nkhani ya kaperekedwe ka makontilakiti.
Mkulu woyang’anira ntchito za Hivos mdziko muno a June Kambalametore anati dziko lino likutaya ndalama zambiri kudzera mu katangale ndi njira zina zowonongera ndalama za boma kudzera mukugula katundu ndi zinthu zosiyanasiyana.
Iwo anapempha atolankhani mdziko muno kuti akhale ndi chidwi kutsata njira zomwe makontilakiti ochitika poyera amakhalira komanso kuzindikiritsa anthu kuti adzitenga nawo mbali pochita kalondolondo wa zinthu yemwe akuchitika ku dera kwawo.
“Gawo loposa theka la ndondomeko ya chuma imapita ku nthambi yogulira katundu (procurement), koma ndalama zambiri zimawonongeka chifukwa cha katangale ndi ziphuphu.
Tikupempha atolankhani kuti muyikepo chidwi pozindikiritsa anthu komanso kufukula mwakuya nkhani zokhudza kagulidwe ka zinthu ka boma ndi nthambi zake,” anatero a Kambalametore.
Joel Ching’ani yemwe ndi wachiwiri kwa mkulu wa OC-MSG anagwirizana ndi zomwe ananena a Kambalametore kuti njira zomwe zimatsatidwa pogula zinthu zikuwonongeka kaamba ka katangale.
“Atolankhani akuyenera kutsatira njira zonse zogulira katundu komanso kutenga nawo mbali pochita kalondolondo komanso kumasulira zomwe zikuchita zokhudza kapa-tsidwe ka kontilakiti kwa anthu,” anatero a Ching’ani.
Sam Kambani, m’modzi mwa ochita kafukufuku ku bungwe lothana ndi katangale komanso ziphuphu (Anti Corruption Bureau) mchigawo cha kum’mawa anati kuti atolankhani adzilemba bwino nkhani zokhudza katangale yemwe amachitika nthawi yogula katundu, iwo akuyenera kukhala ndi upangiri wa mmene njirayi imakhalira komanso kupeza anthu oyenenera omwe angawapatse zinthu zomwe amafuna.
“Ngati njirayi simungayimvetse ndikovuta kulemba nkhani zomwe zimachitika pogula katundu ndi kaperekedwe ka makontilakiti,” anatero a Kambani.
Hivos inachititsa maphunzirowa ndicholinga chofuna kusula atolankhani pa nkhani yofufuza mwakuya mmene zimakhalira pankhani yogula zinthu.