MkwasoNkhani Zina

Atuluka DPP posakhutira ndi chisankho cha chipulula

Anthu awiri omwe anali ndi maudindo mchipani cha Democratic Progressive (DPP) atula pansi ma udindo awo kaamba kosakhutira ndi kupambana kwa a Damson Chelewani pa chisankho cha chipulula ku dera la pakati m’boma la Mulanje.

Gavanala wa chipanichi a Elizabeth John ndi gavanala wa ku dera a Vasco Mondiwa atula pansi maudindowa ponena kuti chisankho cha chipulula chomwe chinachitika pa 23 Epulo sichinayende bwino.

Kalata yomwe awiriwa alemba akudzudzula utsogoleri wa chipanichi posamva madandaulo omwe analipo ngakhale omwe amapikisana pa chisankhochi anapititsa umboni okwanira.

Koma kalata yomwe analemba mkulu woyendetsa chisankho mchipani cha DPP a Jean Mathanga inatsimikiza zakupambana kwa a Chalewani womwe anapambana atagonjetsa a Rhoda Gadama Misomali, a Aaron Chambo, a Izeck Brazil, ndi a Mphatso Gadama Nankhoma.

A Rhoda Gadama ati iwo ayima ngati phungu woyima payekha chifukwa ali ndi maziko okhazizika komanso kaamba ka zitukuko zomwe akhala akuchita ngakhale asali phungu.