Aulumali amenyere maufulu awo — FEDOMA
Bungwe la Federation of Disability Organisations in Malawi (FEDOMA), lati nkofunikira kwambiri kuti anthu amene ali ndi ulumali muno mu Malawi ayambepo kulankhula pa zinthu zimene zikuwapsinja komanso kutengapo mbali pa chitukuko cha dziko lino pokhala m’maudindo osiyanasiyana.
A Ethel Kachala, omwe ndi mkulu wa mapologalamu ku FEDOMA, alankhula izi Lachiwiri pa 4 Febuluwale 2025, pomwe amadziwitsa khonsolo ya Balaka za pulojeketi yawo yomwe ikulimbikitsa anthu aulumali kuti asamasalire pa zochitika m’madera awo komanso kuti azithanso kukhala m’maudindo osiyanasiyana m’madera awowo.
“Pulojekiti yomwe timadzaidziwitsa khonsolo ya Balaka ndi yoonetsetsa kuti aulumali akutengapo mbali pa zochitika m’madera awo. Takhala tikuigwira kwa miyezi 18 m’maboma a Balaka, Ntcheu ndi Zomba. Kuno ku Balaka pulojekitiyi inali m’mdera a Mfumu Sawali, Mfumu Kalembo komanso Mfumu Nsamala.
“Pano tabweranso ndi pulojekitiyi ndipo tapatsidwa madera a mafumu atatu – kwa Mfumu Phalula, Mfumu Chanthunya komanso Mfumu Phimbi. Takonzeka kugwira ntchitoyi ndi boma, mabungwe kudzanso anthu osiyanasiyana kuti anthu aulumali asatsalire pomwe tikusankhana maudindo kwa anthu osiyanasiyana,” anatero a Kachala.
Iwo ati ndi cholinga cha pulojekitiyi kuonetsetsa kuti amayi, asungwana, abambo ndi anyamata aulumali akuima ndi kulankhula mosaopa za maufulu awo amene ena akuwaphwanyira.
“Aulumali aphunzire kulankhula kapena kupereka malipoti kwa adindo pamene maufulu awo aphwanyidwa. Amene ukumva kuwawa ndi amene umatha kulankhula bwino za m’mene ukumvera osati kudikira munthu wina wapambali kuti akulankhulire,” anatero a Kachala.
A Kachala apitiriza kufotokoza kuti pamene pakuchitika ziganizo zosiyanasiyana pakuyeneranso kukhala aulumali kaamba koti ziganizo zina zimakhuza anthuwa “ndipo zikachitika mosawaganizira zimabweretsa mavuto kwa anthuwa.”
Mkulu woona ntchito zokhuza aulumali ndi okalamba mu khonsolo ya Balaka, a Stanley Chisi, ati ndiokondwa ndi mapulojekiti amene akubwera ndi cholinga chofuna kutukula miyoyo ya aulumali — maka pa nkhani yowaika m’maudindo, amene mwa zina, amachita ziganizo kuyambira kumudzi.
“Kwa nthawi yaitali aulumali akhala akuponderezedwa mu njira zosiyanasiyana. Ndi cholinga cha boma ndi mabungwe amene amagwira nawo ntchito kuti aulumali akwale ndi mwai wokhala m’maudindo ngati wina aliyense.
“Zambiri zasintha tsopano ndipo aulumali akutenga nawo mbali pa zitukuko komanso popereka maganizo awo ndi kupanga nawo ziganizo. Komabe ntchito idakalipo kuti zinthu zifike pabwino chifukwa ambiri sapatsidwa mpata wotula nkhawa zawo kwa adindo ndi kwina,” anatero a Chisi.
Iwo ati aulumali ambiri akusowa mwai wa maphunziro ndi zitukuko zina kaamba kakusowa kwa ndalama kuti afikiridwe m’madera amene akukhala — ndipo ena amakhala kutali kwambiri ndi kumene angapeze maphunziro ndi thandizo lina lofunika pa moyo wawo.
A Chisi akuti anthu ndi mabungwe akufuna kwabwino athandizepo kuti mapulojekiti monga imene a FEDOMA akugwira kuti anthu aulumalira asasalire m’mbuyo pa ntchito zosiyanasiyana.
“Anzathuwa amasowa zambiri pa moyo wawo monga njinga, zipangizo zothandiza kuti azimva ndi zina zambiri. Choncho pambali powathandiza kuti akhale nawo m’maudindo komanso kuti azitha kulankhula pa mavuto omwe akukumana nawo, tiyeneranso kuwathandiza ndi zipangizozi,” anatero a Chisi.
A FEDOMA akugwira pulojekitiyi m’maboma a Balaka, Ntcheu Zomba ndi Kasungu, ndi thandizo lochokera ku Brot ku Germany.