News

Bajeti ibalanji?

Nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda yafika ku Nyumba ya Malamulo komwe ikuyembekezeka kupereka ndondomeko ya chuma ya 2025-2026.Amalawi ali ndi chidwi kuti amve ngati ndondomeko ya chumayi mukhale zinthu zomwe zingakweze chuma cha dziko lino komanso mmene angathanirane ndi mavuto a zachuma omwe ayanga dziko lino.Kwa ogwira ntchito m’boma, nawo maso ali ku njira kuti awone ngati mu bajetiyi mukhale gawo lowakwezera malipiro malingana ndi bungwe lomwenyerera ufulu wa ogwira ntchito m’boma la Civil Servants Trade Union (CSTU).Akuluakulu a bungweli anawopseza kuti ogwira ntchito m’boma anyanyala ntchito ngati boma silikweza malipiro awo momwe iwo akufunira.Zokambirana pakati pa magulu awiriwa masiku apitawa sizinaphule kanthu pamene CSTU inabweza akuluakulu aku boma kuti gawo la ndalama zomwe anati awonjezera linali lochepa kotero iwo ali chile kuti amve ngati gawoli alikweza.