General

Bamusi, Pankuku adutsa moyera pa zisankho za chipulula za DPP

Wolemba: Rose Chipumphula Chalira

A John Jackson Bamusi ndi a Jonah Pankuku ndiamene adutsa moyera pa zisankho za chipulula za chipani cha Democratic Progressive (DPP) Lachiwiri m’boma la Balaka.

A Bamusi womwe analipo wapampando wa mabungwe omwe siaboma m’bomali apambana ndi mavoti 359 ku dera la Balaka Ngwangwa pomwe a Mwayiwawo Nambeza sanapeze voti iliyonse.

Mdera la Balaka Bwaila, yemwe anali mtolankhani wodziwika bwino ku nyumba yowulutsa ndi kusindikiza nkhani ya Times a Pankuku ndiwomwe adzayimire chipani cha DPP ngati phungu wa Nyumba ya Malamulo atapeza mavoti 177, a Prince Mulumbe 97, a Mercy Dosa 26 pomwe a Innocent Banda 16.

Mu chisankho cha makhansala, a Tiyanjane Chisowile ndiamene apambana mu Wodi ya Mchengawede atakwanitsa kupeza mavoti 128, kugonjetsa a Brian Chimenya omwe anapeza mavoti anayi, a Sanwedi Vito omwe anapeza mavoti 6 komanso a Emma Kaduma omwe anapeza mavoti 24.

Dera la Balaka Ngwangwa ndi latsopano chigawireni madera a aphungu.