‘Bukushopu ilimbikitsa chikhalidwe chowerenga’

Bukushopu yaku Kasungu

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Montfort Media Limited yomwe imasindikiza mabuku ndi kugulitsa katundu osiyanasiyana inakhazikitsa thambi yake m’boma la Kasungu ngati njira imodzi yolimbikitsa anthu ozungulira bomali kupeza katundu mosavuta.

Mkulu woyang’anira maphunziro m’bomali a Isabel Mwage anati kubwera kwa nyumbayi kuthandiza kubwezeretsa chikhalidwe chowerenga chifukwa muli mabuku okomera wina aliyense komanso ophunzitsa.

“Ophunzira sukulu za sekondale ndi ena azipeza zinthu zofunikira mosavuta komanso pa mtengo wa-bwino kusiyana ndi kale pomwe anthu amayenda mtunda wautali kukagula mabuku ophunzitsa ndi ena mu mzinda wa Lilongwe,” anatero a Mwage.

Iwo anati chikhalidwe chowerenga mabuku osiyanasiyana chinatha ndipo kubwera kwa bukushopuyi kuthandiza kubwezeretsa chikhalidwechi mchimake.

Mwage: Ophunzira azipeza zinthu zawo mosavuta

“Kubwera kwa bukushopu kuno kuthandiza anthu kukhala ndi chidwi chowerenga chifukwa muli mabuku osiyanasiyana ophunzitsa zinthu,” anatero a Mwage.

Iwo anapempha anthu a m’bomali kuti asamalire malowa ndi kuwagwiritsa ntchito moyenerera.

Mfumu Kazombo inati ndikoyamba m’bomali kukhala ndi nyumba yogulitsa mabuku komanso katundu osiyanasiyana pa mtengo wabwino.

“Bukushopuyi ithandiza anthu kudziwa zinthu zosiyanasiyana chifukwa muli mabuku a mtundu wina uliwonse komanso zinthu za mpingo wa chikatolika,” anatero a Kazombo.

Mfumuyi inati anthu ake tsopano azipeza zinthu mosavuta komanso malowa athandiza kuzamitsa chikhalidwe chowerenga pakati pa anthu.

Mkulu wa Montfort Media Bambo Blaise Jailosi anati ndicholinga cha kampaniyi kutukula ntchito zolimbikitsa kuwerenga komanso kusindikiza mabuku osiyanasiyana.

“Cholinga chathu tikufuna anthu azipeza zinthu zofunikira pa moyo wawo mosavutikira komanso kufuna kulimbikitsa akhristu kuti azipeza zinthu za mu mpingo mosavuta,” iwo anatero.

Iwo anapempha anthu a m’bomali kuti akhale ndi umwini ogwiritsa ntchito malowa pogula katundu yemwe akugulitsidwa pa mtengo wabwino.