General

Bungwe la MEC ndi lomwe liulutse zotsatira zovomerezeka – Mtalimanja

Wolemba: Joseph Kayira

Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lapempha onse omwe anapikisana pa chisankho cha pulezidenti, aphungu a Nyumba ya Malamulo ndi makhansala, kuti asunge bata ndi kudikirira zotsatira zochokera ku bungweli osati zomwe anthu ena akutulutsa ndi kuzilengezetsa m’masamba a mchezo.

Wapampando wa bungwe la MEC, a Annabel Mtalimanja, ati iwo agwira ntchito motsatira malamulo ndipo ayesetsa kuti zotsatira za chisankho ziunikidwe ndi kuonkhezedwa mwachilungamo.

Mtalimanja: Tiloleni tigwire ntchito yathu momasuka (Chithunzi: Internet)

“Tiloleni kuti tigwire ntchito yathu momasuka. Musatifulumizitse chifukwa kutero ndi kutiwonongetsa ntchito. Zomwe anthu ena akulengezetsa ndizosatsimikizika. Malamulo amatipatsa ife mphamvu yoyendetsa chisankho mwaukadaulo ndi motsata malamulo. Tiyeni tisunge bata ndi mtendere kuti ntchito yonse imene MEC ikugwira iyende bwino.

“Tiyeni tonse titengepo gawo ndi mbali kuti Malawi apitirire kukhala dziko la mtendere. Tisafotokozere anthu kuti tapambana pamene zotsatira sizinatuluke. Pakanali pano palibe amene wapambana chifukwa ife sitinalengeze wopambana. Mawu ali ndi mphamvu; azipani ndi okutsatirani yankhulani moyenerera ndi momangirira. Pakali pano aliyense akufuna kumva zotsatira koma zotsatira sizingatuluke ntchito isanathe,” anatero a Mtalimanja.

Iwo apemphanso nyumba zoulutsa mawu komanso anthu amene amaika nkhani m’masamba a mchezo kuti asalole kugwiritsidwa ntchito ndi anthu ena kuti asokoneze bata.

Akuluakulu a MEC kuchititsa msonkhano wa atolankhani ku Lilongwe (Chithunzi: MEC)

Andale ena akhala akuchititsa misonkhano kapenanso kuponya zotsatira mmasamba a mchezo kuti apambana chonsecho bungwe la MEC silinayambe kulengeza zotsatira. A Mtalimanja afotokoza kuti malamulo amati zotsatira za pulezidenti ziulutsidwe pakatha masiku asanu ndi atatu. Malamulo amanenanso kuti zotsatira za chosankho cha phungu ziulutsidwe pakatha masiku 14 ndipo zotsatira za chisankho cha khansala ziulutsidwe pakatha masiku 21.