Environment

CHENJEZO LA CHIOPSEZO CHA NAMONDWE WOTCHEDWA CHIDO

Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi (DODMA) ikudziwitsa anthu onse kuti malipoti ochokera ku Nthambi Yoona Zanyengo, atsindika kuti Namondwe Chido, yemwe akuyenda m’nyanja ya mchere (Indian Ocean) wakula mphamvu ndipo akuyembekezeka kuwomba pa gombe/doko la Nacala m’dziko la Mozambique Lamulungu pa 15 December. Doko la Nacala liri pa mtunda wa makilomita 500 ndi boma la Mulanje ndipo pachifukwachi, kuwomba kwa namondweyu ku Nacala kutha kudzetsa mvula yochuluka komanso kusefukira kwa madzi m’madera ena a m’dziko muno kuyambira Lamulungu pa 15 Disembala kapena Lolemba pa 16 Disembala.

Pachifukwachi, Nthambiyi ikupempha kuti titsatire malangizo awa kuti titeteze miyoyo:
Tisazengereze, tisakakamire, tiyeni tisamukire mmadera a kumtunda.

Tionere, kumvera komanso kuwerenga uthenga wa za nyengo kuti tidziwe momwe nyengo ikhalire m’dera lathu.

Tipewe kuwoloka mitsinje yosefukira komanso kuyenda mmadera omwe madzi asefukira. Madzi angachepe bwanji, ali ndi kuthekera kotikokolora.

Tisayandikire mawaya a magetsi, tidziwitse msanga a ESCOM, amfumu kapena a polisi za mawaya kapena mapolo a magetsi omwe agwa.

Tisathamangire kupulumutsa katundu yemwe akukokoloka ndi madzi, tionetsetse kuti moyo wathu ndi wa ena ngotetezeka.

Tisamutsiretu katundu yense wofunikira ku malo okwera.

Ngati tingakwanitse, tipereke thandizo loyambilira (first aid) kwa ovulala ndipo tipite nawo kuchipatala mwansanga.

Padakali pano, DoDMA ikuyang’ana mwatcheru za chenjezoli ndipo yadziwitsa kale makomiti ogwira ntchito zosiyanasiyana (clusters) kuti akhale tcheru komanso kuchita machawi pokonzekera za namondweyu.

Nthambiyi yaikiratu zipangizo zothandiza kupulumutsa anthu omwe angakhudzidwe komanso kudziwitsa othandiza kupulumutsa anthu pangozi monga asilikali a Malawi Defence, Force, Malawi Police, Marine Department komanso Malawi Red Cross Society kuti akhale okonzeka kukagwira ntchito mmadera omwe ali pachiopsezo chokhudzidwa.

Nthambiyi yadziwitsanso akuluakulu a mmakhonsolo komanso ma komiti oona za ngozi zogwa mwadzidzidzi kuti akhale tcheru ndi kudziwitsa anthu mmadera mwawo komanso kuwathandiza kusamukira mmithawira (evacuation centres).

DoDMA ikugwiranso ntchito ndi Nthambi Yoona za Nyengo kulengeza mauthenga omwe akulunjika za mmene anthu angapewere komanso kuchepetsa chiopsezo chokhudzidwa ndi zotsatira za namondweyu.

Ndi Udindo Wa Aliyense Kuchepetsa Chiopsezo Cha Ngozi Zadzidzidzi!

Zithunzi zikuonetsa kuonongeka kwa nyumba zomwe posachedwapa zakhudzidwa ndi mvula yamphamvu mmadera ena mdziko muno.