Uncategorized

Chipatala cha Karonga chiyamikira thandizo la NICE

Chipatala chachikulu cha Karonga chayamikira bungwe la National Initiative for Civic Education (NICE) Trust pothandizira kuti anthu azilandira chisamaliro chabwino m’bomali kudzera mu ndondomeko yakagwiridwe kabwino kantchito.

Mkulu wa zaumoyo m’bomali a Clement Gonthi, anati m’mbuyomu ofesi yawo idali ndi ndondomeko yakagwiridwe ka ntchito yotchedwa service charter pachingerezi koma idatha ntchito. Bungwe la NICE lidathandizira ofesiyi kupita ku Ntchisi komwe adakaphunzira kuchitanso ndondomeko zawo zatsopano.

A Gonthi anati ndi chithandizo cha bungweli, ofesi yawo idakhazikitsa ndondomeko yatsopano imene kenako adaimasulira mu Chichewa, Chitumbuka ndi Chingonde ndikuzigawa.

“Ndondomekozi zimauza anthu zomwe akuyenera kuyembekezera kuchokera kwa anthu ogwira ntchito komanso panthawi yomweyo, ikuonetsa zimene akuyenera kuchita ngati anthu amene akuyenera kulandira thandizo pachipatala,”  iwo anatero.

Gonthi: Munthu wodziwa ndi wabwino

A Gonthi anati poyamba, ndondomeko zimenezi zimangolengezedwa kwa ogwira ntchito basi, zomwe zikutanthauza kuti anthu ofuna chithandizo cha mankhwala samadziwa ufulu ndi udindo wawo pamene abwera kuchipatala.

“Mtundu wodziwa ndiwabwino chifukwa zomwe akudziwazo zimawathandiza kufunsa kuti athandizidwe moyenera kuchokera kwa ogwira ntchito kuchipatala. Panthawi yomweyo, ngati antchito athu adziwa kuti anthu akuzindikira zomwe ife tikuyenera kuwachitira, Nthawi zonse amagwira ntchito bwino. Ndondomeko zakagwiridwe kabwino kantchito ndi chida chathu,” anatero a Gonthi.

Malinga ndi a Gonthi, bomalo liri ndi zipatala zokwana 21 zomwe zikutumikira anthu pafupifupi 364,000. Chipatala chachikulu cha Karonga chili ndi mabedi 208.

Mkulu wa bungwe la NICE m’bomali a Christabel Munthali, anati bungwe lawo linaganiza zothandizira kukonza ndondomeko zakagwiridwe kantchito atazindikira kuti anthu samadziwa mmene zipatala ziyenera kugwirira ntchito, motero ufulu wa anthu umaphwa-nyidwa ndipo kuti pena anthu amayembekezera zinthu zambiri kuchoka kwa ogwira ntchito.

“Molingana ndi polojekiti imeneyi, cholinga chathu ndikupereka mauthenga kwa anthu kuti azitha kupempha chisamaliro chimene akuchifuna komanso kupanga kuti ogwira ntchito azigwira mwaukadaulo,” iwo anatero.

A Munthali anaonjezera kuti kupatula zaumoyo, bungwe la NICE m’bomali likuphunzitsa anthu pantchito zosiyanasiyana zachitukuko kuti mzika zizidziwa ufulu ndi udindo wake.