MkwasoUncategorized

Chiwerengero cha omwalira ndi namondwe Chido chifika 7

Nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi yalengeza kuti chiwerengero cha anthu omwe amwalira ndi namondwe wa Chido tsopano chafika pa asanu ndi awiri (7).

Malingana ndi chikalata chomwe nthambiyi yatulutsa lero (Lachiwiri), boma la Salima ndilomwe kwamwalira anthu ambiri okwanira atatu pomwe ku Kasungu, Machinga, Blantyre komanso Lilongwe kwamwalira munthu mmodzi.

Chikalatachi chomwe wasayinira ndi komishonala wa nthambiyi a Charles Kalemba chatinso anthu pafupifupi 34,741 ndiomwe akhudzidwa ndi namondweyu pamene nyumba zokwanira 7,721 ndizomwe zaonongeka pomwe anthu khumi ndi asanu ndi mmodzi (16) ndiamene avulala.

Pakadalipano, nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidziyi yati iyo ndi mabungwe ena akupanga njira zoti athandizire anthu omwe akhudzidwa ndi namondweyu yemwe watha dzulo Lolemba.

Namondweyu yemwe anachokera ku nyanja ya mchere ya Indian ndi kudutsira mdziko la Mozambique anakhudza kwambiri maboma monga Balaka, Blantyre, Chikwawa, Chiradzulu, Kasungu, Lilongwe, Machinga, Mangochi, Mchinji, Mulanje, Neno, Mwanza, Thyolo, Zomba, Ntcheu, Phalombe ndi Salima.