Environment

CycloneChido

Unduna wa Zamaphunziro walengeza za kuyimitsidwa kwa maphunziro a pulayimale ndi sekondale m’maboma omwe akuyembekezeka kukumana ndi chiopsezo cha Namondwe wotchedwa Chido yemwe wafika dziko dziko muno ndi mphepo.

Kalata yomwe wasayinila mlembi ku Undunu a Rachel Chimbwete ati makalasi a mawa ndi omwe atakhudziwe kutsatira mphepo ya Namondwe yu. Malingana ndi uthenga wochokera ku undunawu sukulu zomwe sapita mawa ndi zochokera m’maboma awa Mangochi, Machinga, Zomba, Mulanje, Phalombe, Neno, Mwanza, Dedza, Ntcheu, Balaka,Thyolo, Blantyre,Chiradzulu, Nsanje komanso Chikwawa.