DPP yakonzeka kulamulanso– Muntharika
Wolemba: Rose Chipumphula Chalira
Pulezidenti wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP), a Arthur Peter Mutharika ati chipani chawo ndi chokonzeka kulamuliranso dziko lino.
A Mutharika ayankhula izi lero pomwe anachititsa msonkhano wa atolankhani kunyumba kwawo m’boma la Mangochi.
M’mawu awo iwo ati ndi okonzeka kutenganso mpando wa pulezidenti pa chisankho chomwe chichitike chaka cha mawa.
“Ine ngati Peter Mutharika, ndine wokonzeka kutsogolera chipani cha DPP ndi kupambananso ndi mavoti ochuluka kachikena pa chisankho cha mu 2025,” atero a Mutharika.
Mutharika: Tikutenganso boma (Chithunzi: Internet)
Iwo atinso pali anthu ena omwe akufuna kubweretsa lamulo loti iwo asadzayimire kamba kaamba ka zaka zawo. Koma iwo ati izi sizitheka ndipo iwo adzayimira chipani cha DPP m’chaka cha 2025.
A Mutharika afotokozanso kuti ndiwokhumudwa kuti chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chikubweretsa ulamuliro wankhaza m’dziko muno monga momwe zinaliri mu nthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi. Iwo atsindika mfundoyi potchula za kumenyedwa kwa otsatira chipanichi mu mzinda wa Lilongwe sabata ziwiri zapitazo.
A Mutharika atinso dziko lino lilibe mtsogoleri: “Kuyambira lero kudzafika mwezi wa Seputembala chaka chamawa ndizilankhula ndi Amalawi pafupipafupi pofuna kulimbikitsana nawo pa mavuto omwe akukumana nawo kaamba kakulephera kwa boma la mgwirizano wa Tonse,” atero a Mutharika.
“Ndikuwawuza a Chakwera kuti sangatukule dziko lino pochita nkhanza kwa anthu ndikulimbikitsa za zipolowe. Anthu akufuna utsogoleri osati nkhanza zanuzo. Nkhanzazo sizingathetse mavuto omwe Amalawi akukumana nawo pano, monga njala komanso kusowa kwa chiphaso choyendera kupita mayiko akunja,” atero a Mutharika.
Iwo atinso kumenyedwa kwa otsatira chipani cha DPP mu mzinda wa Lilongwe ndizomvetsa chisoni ndipo sizokufunika mu nthawi ya zipani zambiri komanso mu ulamuliro wa demokalase.
A Mutharika ati ndi odabwa kuti mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera, omwenso ndi pulezidenti wa chipani cha MCP, sakubwera poyera ndikudzudzula za upandu zomwe mamembala otsatira chipani chawo anachita.
A Mutharika ayamikira mabungwe omwe siaboma, amipingo ndi zipani zina za ndale omwe anadzudzula za mchitidwewu.
“Ndikuchenjezeni a chipani cha MCP kuti nthawi yanu yatha. Mukuyambitsa ziwawa kwa otsatira chipani cha DPP ndipo mudzalandira dipo pa zomwe mukuchitazi. Ndipo musiye zomwe mukuchitazi chifukwa nthawi yanu yatha. Ndikuchenjezeni ndithu a MCP,” anatero a Mutharika.
Iwo anapitiriza kunena kuti chipani cha MCP chikuyenera kulolerana ndi zipani zina kuchita misonkhano yokopa anthu m’dziko muno osati kuwachitira nkhwidzi poyambitsa ziwawa.
Pomaliza iwo ati ali ndi chikhulupiriro choti oyang’anira chisankho a DPP sadzachitidwanso za upandu nthawi ya chisankho ngati m’mene zinachitikira m’chaka cha 2020 nthawi ya chisankho cha chibwereza pomwe anthu ena anasowa.