General

GALU WAKUDA WASAUTSA

  • Madera ambiri alibe chakudya
  • Apempha chilungamo pa kagawidwe ka chimanga
  • Ku ADMARC kulibenso mpumulo

Olemba:

Precious MSOSA ndi Brown MDALLA

Pamene atsogoleri osiyanasiyana adandaula pa za chiopsezo chomwe miyoyo ya anthu        ambiri alinacho kaamba ka vuto la njala, zikuwoneka kuti anthuwa avale zilimbe chifukwa misika yambiri ya nthambi yogula ndi kugulitsa mbewu ya Agricultural Development and Marketing Corporation (ADMARC) kulibenso mpumulo.

Ngakhale masiku apitawa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera analamula kuti misikayi itsegulidwe ndikuyamba kugulitsa chimanga, zinthu sizikuwoneka choncho pomwe m’madera ambiri misikayi idakali yotseka ndipo kwa yomwe ili yotsegula, palibe chiye-mbekezo chilichonse chomwe chikuperekedwa.

Kuwonjezera apo, nayo ntchito yogawa chimanga ku mabanja okhudzidwa ndi njala m’maboma ambiri siyinagwire msewu kweni kweni.

Izi ndi zina mwa zomwe zikubweretsa nkhawa kwa aphungu, mafumu ndi mabungwe ena kuti anthu ambiri atha kumwalira chifukwa cha vuto lakusowa kwa chakudya.

Mwachitsanzo, aphungu ena a Nyumba ya Malamulo a chipani cha Malawi Congress (MCP) adandaula kale za kukula kwa njala m’madera awo kotero apempha boma kuti liyesetse kupeza njira zothanirana ndi vutoli mwa msanga.

M’madera ena, zinthu zafika kale pa mwana wakana phala pamene zikumveka kuti anthu ena ayamba kale kudya mitsitsi ya zomera za kutchire monga nyika, mpama komanso chitedze, mwazina.

Mwachitsanzo, mdera la Mfumu Yayikulu Ntonda m’boma la Ma-ngochi, anthu ambiri akugonera mpama ndipo pali chiopsezo choti ‘zakudyazi’ zikatha, anthu ambiri   agwira njakata chifukwa zikukanganiridwa ndi ambiri.

A Aida John wochokera m’mudzi wa Songa 3 anawuza nyuzipepala ya The Nation ya pa 17 Sepitembala kuti zinthu sizili bwino konse.

“Nkhawa yathu ndiyakuti panopa sitikutha kupeza mpama wokwanira chifukwa dera lonse likukanganirana zomwezi. Sitikudziwa kuti zidzatithera bwanji ‘zakudyazi’ zikadzatha,”        anatero a John.

Nayo Mfumu Yayikulu Ntonda inafotokozeranso nyuzipepala ya The Nation kuti anthu ake akhala akudya mpama kuyambira mwezi wa Epulo chaka chino.

“Zinthu zafika poyipa kwambiri ndipo tikungokhalira chisomo cha Mulungu. Ngati akufuna kwabwino satifikira msanga, tifa ndi njala,” inatero mfumuyi.

Mneneri wa khonsolo ya Mangochi, Bishop Witmos anatsimikiziranso nyuzipepala ya The Nation kuti ndizoona kuti m’madera ena m’bomali vuto la njala lafika povuta kwambiri kotero akuchita kafukufuku wa anthu omwe akhudzidwa omwe akufunikira thandizo mwamsanga.

Ndipo polankhula masiku apitawa pa msonkhano womwe chipani cha Malawi Congress (MCP) chinachititsa pa sukulu ya pulaimale ya Mtunthama m’boma la Kasungu, phungu wa ku Nyumba ya Malamulo mdera la kummawa kwa bomali a Madalitso Kazombo anati vuto la kusowa kwa chakudya lakula kwambiri mdera lake.

Choncho iwo anapempha boma kuchita changu pa ntchito yopereka chakudya kwa anthu okhudzidwa.

Ngakhale a Kazombo anayamikira anthu a m’bomali kuti ndiolimbikira pa ntchito za ulimi, iwo anati vuto la kusowa kwa chakudya labwera kaamba koti anthu sanakolole zokwanira chifukwa cha ng’amba yomwe inakhudza maboma ambiri komanso kukwera kwa mitengo ya zipangizo za ulimi.

“Anthu okhala m’boma lino ndiolimbikira kwambiri pa ntchito za ulimi, koma chaka chino zinthu zawavuta kaamba ka vuto la ng’amba lomwe boma lino linakumana nalo komanso kukwera mtengo kwa fetereza,” anatero a Kazombo.

Naye phungu wa ku Nyumba ya Malamulo mdera la Lilongwe Mpenu, a Jean Sendeza anagwirizana ndi a Kazombo kuti anthu ambiri akusowa chakudya m’dziko muno                kuphatikizapo anthu a dera lake kotero anapempha boma kuyambapo ntchito yogawira anthuwa chakudya.

“Boma linakhazikitsa thumba la padera la ndalama zogulira chakudya choti chigawidwe kwa anthu omwe akuvutika ndi njala. Tsono pempho lathu ndilakuti, boma likuyenera kuchita changu kuyambapo ntchitoyi,” anatero a Sendeza.

M’boma la Balaka, vuto la njala silinasiyenso mpata pomwe madera ambiri akhudzidwanso ndi vutoli. Malingana ndi lipoti lakukonzekeretsa ntchito yogawa chakudya kwa anthu ovutika, anthu 233,101 akhudzidwa ndipo mabanja 51,800 ndiamene akuyembekezeka kulandira thandizoli zomwe mwazina ndi thumba la chimanga limodzi kwa miyezi ingapo.

Madera a Mfumu Yayikulu Kalembo, Amidu, Nsamala ndi Kachenga ndiomwe akhudzidwa kwambiri. M’maderawa, anthu ambiri akudalira kumagayitsa makaka amene akumawasakaniza pang’ono ndi deya nkupanga ufa.

Mu misika ya ADMARC, chimanga chikugulitsidwa pa mtengo wa K790 pa kilogalamu zomwe ndi K39, 500 pa thumba lolemera makilogalamu 50. Kwa anthu ambiri, mtengowu udakali wokwera kwambiri kotero akulepherabe kugula thumbali ndipo ena akumapita kwa mavenda komwe ndichotsikirapo.

Nyuzipepala ya The Daily Times ya pa 17 Sepitembala inati m’madera ena monga ku Mzuzu ndi Blantyre, anthu amagula chimangachi motsikirapo mtengo monga K31,500 pa thumba lolemera makilogalamu 50. 

Anthu okwana 5.7 miliyoni ndiamene ali pa chiopsezo cha njala yadzaoneni m’dziko muno malingana ndi lipoti la Malawi Vulnerability Assessment Committee (MVAC). Mwa anthuwa, ena afuna thandizoli kwa miyezi itatu pomwe ena miyezi isanu ndi umodzi. 

Mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwera akhala akulankhula mobwerezabwereza kuti akudziwa kuti anthu ambiri akusowa chakudya m’dziko muno ndipo boma lawo lichita chotheka kuthana ndi vutoli.