Gule kwawo! Maule atsanzika
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yawona msana wa njira mu mpikisano wa Castel Cup itagonja ndi Mzuzu City Hammers 4-1 pa mapenate atalephera onse kupeza zigoli mu mphindi 90 za masewerowa lero pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.
Zateremu, Mzuzu City Hammers idzachotsana chimbenene ndi Mighty Mukuru Wanderers mu mafayinolo loweluka likubwerali pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.
Maule anataya mipata yambiri imene anakatha kupezera zigoli komanso anyamata a Mzuzu City Hammers nawonso anaonetsa chamuna chifukwa sananjenjemere kuti akumenya ndi timu yaikulu.
Zateremu, Maule atuluka sizoni ya 2024 ndi chikho chimodzi chokha cha Airtel Top 8 chimene anapambana atagonjetsa Silver Strikers pa bwalo la Bingu.
Wolemba: Yankho Paketi
Chithunzi Bullets Facebook page.