Gulu la achinyamata lilimbikitsa maphunziro
Wolemba: Elita MTONGA
Pofuna kutukula maphunziro aachinyamata makamaka atsikana, gulu lotchedwa Imagine 360 Girls Empowerment m’boma la Mangochi lati likufuna kuthandiza atsikana omwe amakanika kupitiriza maphunziro kaamba ka mavuto azachuma.
Mkulu wa gululi a Dorothy Kamenya wati gululi lidayamba pofuna kuthandiza atsikana osowa m’derali kumbali ya maphunziro.
“Kuno ku Mangochi ndikomwe atsikana ambiri amasiyira sukulu panjira, choncho tinaganiza kuti gululi lizithandiza atsikana ngakhale amene anaberekapo kale,” anatero a Kamenya.
Koma iwo anati akukumana ndi mavuto azachuma kotero apempha anthu akufuna kwabwino kuti awathandize kuti khumbo lawo likwaniritsidwe.
“Poyamba timayesera kumaswa miyala ya kware komanso kumaperekera miyala pamalo azomangamanga koma sizi-mathandiza chifukwa pena ndalama samatipatsa. Tinaganiza kuti tizingoyamba kubwereketsa kuti tikamabwezeredwa tizithandizira achinyamatawa koma zinakanikanso,” anatero a Kamenya.
A Kamenya anati ndi khumbo lawo kuona achinyamata aderali akupita patsogolo kumbali ya maphunziro ndicholinga choti adzathe kuziyimira paokha.
“Tikufuna kuti achinyamatawa adzakhale odziyimira paokha,” anatero a Kamenya.
Iwo anapitiriza kuti: “Kupatula ndalama zolipirira kusukulu, kwa ena omwe anasiya sukulu panjira titha kufuna zinthu monga makina osokera kuti athe kuphunzira kusoka, zitenje zoti atha kuphunzira luso lopanga dizaini, makina akompyuta ngakhalenso makamera kuti athe kuphunzira kujambula kuti zidziwathandiza kupeza ndalama.”
Gulu la Imagine 360 Girls Empowerment lidayamba mu Novembala chaka chatha m’mudzi wa Chiwaula, kwa Mfumu Yayikulu Chimwala m’boma la Mangochi.