Uncategorized

‘Katangale, ndale zapha misewu’

Wolemba: Faith Kaisi MATHOTHO

Katswiri wina yemwe amalankhulirapo pa za ulamuliro wabwino, a Moses Mkwandawire omwenso ndi mkulu wa bungwe la Nyika Institute of Governance, wati kusokonekera kwa ntchito zomanganso misewu m’dziko muno, kukudza kaamba ka katangale ndi m’chitidwe wa andale kulowererapo pa chitukukochi – zomwe zachititsa kuti misewu yambiri ikhale yoonongeka ndi yosadalilika.

Ndemanga ya a Mkandawire ikudza pomwe misewu yambiri m’dziko muno, kuphatikizapo waukulu kwambiri wa M1, yaonongeka kwambiri. Mwa chitsanzo mbali ina ya msewu wa M1, waonongeka kwambiri maka pakati pa Blantyre ndi Lilongwe; Lilongwe ndi Mzimba; komanso Mzuzu ndi Karonga. Ngakhale kuti makontiraki-tala ali mkati kukonzanso msewuwu – ntchitoyi ikuyenda mosisitika ndi mosapereka chiyembekezo.

A Mkandawire sanapsatire ponena kuti ziphuphu ndi katangale, yemwe walekereredwa kwa nthawi yaitali, ndi zina mwa zomwe zikuchititsa kuti misewu ya ku Malawi izikonzedwa mwakaphulira.

“Katangale ndi ziphuphu ndi zomwe zikuthandizira kuti ntchito yokonza misewu ibwerere m’mbuyo. Komanso tinene pano kuti kulowelerapo kwa anthu a ndale pa ntchitozi ndi china mwa zifukwa zomwe zatifikitsa pamene tili leropa. Andale athu akuyenera kuyamba kukonda dziko lawo ndikuthandiza kuti ndalama za misewu zisapitirire kuonongeka.

“Makontirakitala amatha kulekeleredwa ndi adindo oyang’anira ntchito za misewu ndipo mapeto ake ndi misewu yosalimbayi. Ntchito yokonza msewu imadya ndalama zambiri   ndipo sibwino kuti makontirakitala azichita utambwali. Utambwaliwu umabwera chifukwa woyang’anira ntchitozi saikapo chidwi,” anatero a Mkandawire.

Misewu yambiri yafika pamenepa (Chithunzi: Dr Matthews Mtumbuka’s Facebook Page)

Mkuluyu wati utsogoleri wa panowu utengereko chitsanzo cha malemu Ngwazi Dr Hastings Kamuzu Banda, mtsogoleri woyamba wa dziko lino, yemwe mu ulamuliro wake anamanga misewu yolimba kwambiri, ina mwa iyo mpaka pano siinawonongekebe – poyerekeza ndi yomwe yamangidwa mzaka zaposachedwapa.

“Ngati dziko tikuyenera kuphu-nzirapo kanthu pa misewu yomwe inamangidwa nthawi ya malemu Ngwazi Kamuzu Banda. Iyeyutu samachita moyerekeza akafuna kumanga misewu. Ma kontirakitala amamanga zolimba, ndipo izi ndi zomwe zathandiza kuti misewu yomwe inamangidwa mu nthawi yake, tikhale nayo mpaka lero. Pakufunika kuikapo mtima pa ntchito za misewu kuti tisamabwererenso ku ntchito yomweyomweyo pakangotha zaka ziwiri. Boma likuwononga ndalama zochuluka koma chitukuko sichioneka chifukwa cha katangale ndi ntchito ya kaphulira,” a  Mkandawire anatero.

Popitiriza, a Mkandawire anati pakali pano ati ndikovuta kuti boma likwanitse kumanga misewu yonse yomwe yaonongeka chifukwa cha ndalama zochepa zomwe zaikidwa mu ndondomeko ya za chuma ya chaka cha 2026/27 ku gawo la zomangamanga.

Kupita chitsogolo, a Mkandawire anati pofuna kuthana ndi vuto la kuonongeka kwa misewuyi, dziko la Malawi likuyenera kumapanga katundu wochuluka wokagulitsa ku misika yakunja ndi cholinga choti lithe kupeza ndalama za kunja (forex) zomwe zingathandize pogula zipangizo zomangira ndi kukonza misewu.

“Komanso ndikofunika kuti Amalawi aphunzire kupereka misonkho mwa chilungamo chifukwa ndi misonkho yomweyi imene ingathandizenso pa ntchito zokonzanso misewu yathu,” anatero a Mkandawire.

Mkandawire: Tiyeni tikonde dziko lathu (Photo Credit: Internet)

Pofika pa 31 December 2025, makilomita 20 okha ndi omwe anakonzedwa pa ma kilomita 80 omwe anaikidwa mu pulojekiti yokonza ndi kumanga misewu. Makilomita 20 omwe anakodze-dwawa anali a misewu ya Lirangwe-Chipini ndi Rumphi-Nyika. Koma misewu yonse yomwe imayenera kuko-nzedwa inali ya Ntcheu-Tsangano Phase 2, Chitipa-Ilomba, Rumphi-Nyika, Linthipe-Lobi, Dzaleka-Ntchisi-Malomo,Chimwaza Nambuma, mlatho wa Thuchira, Chiringa-Muloza, Mtangatanga, Eswazini-Mtantha ndi Embangweni-Edingeni-Engalaweni.

Pafupifupi m’maboma onse muli misewu yoonongeka kwambiri yo-mwe ikuika miyoyo ya Amalawi pa chiopsezo. Malinga ndi nthambi yowona za pa nsewu (Directorate of Road Traffic and Safety Services), mu chaka cha 2025 anthu okwana 1,034 ndi omwe anataya miyoyo yawo chifukwa cha ngozi zapa msewu kuphatikizirapo 401 oyenda pansi komanso 162 oyendetsa njinga.

Malinga ndi lipoti la zachuma la Malawi 2026, ntchito zomangamanga mu chaka cha 2025 zinakwera ndi 5.6% kusonyeza kutsika kwa ntchitozi chifukwa cha kusowa kwa ndalama za kunja komanso kukwera kwa mitengo ya katundu (inflation). Malinga ndi ndondomeko ya chuma ya chaka cha 2026/27 mu chaka cha 2026 ntchitozi zikwera ndi 4.8% ndipo mu chaka cha 2027 zikuye-mbezereka kukwera ndi 5.0%.

Ndalama zokwana K26.5 biliyoni ndi zomwe zinaikidwa mu pulojekitiyi koma chifukwa cha mavuto azachuma mu ndondomeko ya chuma ya 2023/24 ndi 2024/25, ntchitozi zinaima kupangitsa kuti nthambi yokonza misewu ipitilize ntchitozi.