Katemera wa kolera ndiwothandiza – Kandodo-Chiponda
Wolemba: Joseph Kayira
Nduna ya Zaumoyo, a Khumbidze Kandodo Chiponda, yati katemera wa matenda a kolera yemwe tsopano anthu ayamba kulandira m’maboma ena ndiwothandiza kwambiri ndipo ndunayi yalimbikitsa anthu kuti akalandire katemerayu yemwenso alibe vuto lirilonse mthupi mwa munthu.
Ndunayi imalankhula izi Lolemba pa 20 Januwale pomwe imakakhazikitsa ntchito yogawa katemerayu pa chipatala chaching’ono cha Dziwe m’boma la Balaka. Iyo yati boma la Balaka ndi limodzi mwa maboma amene amakhuzidwa kwambiri ndi matenda a kolera ndipo boma, kudzanso mabungwe amene limagwira nawo ntchito, achita chotheka kuonetsetsa kuti matendawa sakufala.
A Chiponda kulankhula kwa anthu omwe anasonkhana pa mwambowo (Chithunzi: Joseph Kayira)
“Pali maboma monga Balaka, kumpoto kwa Mzimba, Karonga, Machinga ndi ena, komwe matendawa amasautsa nthawi zambiri. Kubwera kwa katemera yemwe takhazikitsa lero ndi chitsimikizo choti boma likuyesetsa kuti lithane ndi matendawa. Tikupempha anthu kuti akhale ndi ukhondo m’nyumba zawo. Banja lirilonse likhale ndi chimbudzi komanso lidzimwa madzi aukhondo ophitsidwa komanso kuthira mankhwala popewa matenda otsegula m’mimba komanso kolera amene,” anatero a Chiponda.
Iwo apempha makolo kuti atengere ana awo ku chipatala kuti akalandire nawo katemerayu chifukwa ndiwothandiza kwambiri pa nkhani yolimbana ndi kolera. Amene walandira katemerayu amakhala wotetezedwa kwa miyezi isanu ndi umodzi (6).
A Chiponda ati anthu a chiwerengero cha 75 ndi omwe anadwala matendawa ndipo atatu anamwalira m’boma la Balaka. Boma la Malawi lalandira katemera 770 yemwe wagawidwa m’maboma amene kolera amavuta kwambiri kuchokera ku bungwe la zaumoyo pa dziko lonse la World Health Organisation (WHO) komanso ndi thandizo lina lokuchokera ku bungwe la UNICEF.
Ndunayi yayamikiranso anthu ogwira ntchito zachipatala chifukwa chosatopa pothandiza anthu amene akhuzidwa ndi matenda a kolera m’bomalo.
“Musatope ndi ntchito yabwino imene mukugwira. Sikwapafupi kuthandiza munthu amene akudwala kolera koma inu mumaziperekabe. Komanso yesetsani kutengera katemera wa kolera pena paliponse kuti titeteze miyoyo ya anthu,” anatero a Chiponda.
Boma la Malawi, kudzera mu ndondomeko ya National Cholera Control Plan, likufuna kuthana ndi matenda a kolera pomafika mchaka cha 2030.
M’modzi wa akuluakulu a ku WHO kuno ku Malawi, a Dr Akosua Ayisi anati ndi cholinga cha bungwe lawo kuonetsetsa kuti ntchito za umoyo zikufikira onse amene akudzisowa.
A Ayisi anati bungwe la WHO mogwirizana ndi boma la Malawi, linakhazikitsa ndondomeko zomwe zikuthandiza kuti matendawa asafalikire.
“Ndi thandizo la ndalama lochokera ku WHO tikugwira ntchito yotumiza katemerayu komwe akufunika. Sitikufuna kuti munthu wina atsalire m’mbuyo pa ntchitoyi. Tikufuna anthu alandire katemerayu kuti akhale ndi umoyo wathanzi,” anatero a Ayisi.
Iwo anati ndikofunikira kuti akufuna amayi alandire katemerayu ndipo atengerenso ana awo kuchipatala kuti akalandire katemerayi ngati njira imodzi yolimbikitsira umoyo wathanzi m’mabanja awo.
A Ayisi ati ndi cholinga chawo kuwonetsetsa kuti kolera, asafalikire monga m’mene zinalili mchaka cha 2023 pomwe matendawa anakhudza komanso kupha anthu ambiri. Pamene namondwe wotchedwa Freddy anakhudza dziko lino, anakoledzeranso matenda a kolera ndipo and oposa 40,000 anadwala matendwawa ndipo oposa 1,000 anamwalira ndi kolera.
Mayi James: Mwana wanga anadwala kolera ndipo zinali zoopsa (Chithunzi: Joseph Kayira)
M’modzi wa amayi omwe mwana wawo anadwalapo matenda a kolera chaka chatha, a Patuma James a zaka 55, anati katemera wa kolera amulandira ndi manja awiri.
“Mwana wanga anadwala kolera chaka chatha ndipo matendawa ndiosautsa. Palibe chimene chimayenda matenda akafika pakhomo. Kwa ine katemerayu ndiwofunika kwambiri. Ine nditamva za katemerayu ndinathamangira ku chipatala kuti ndizalandire nawo. Apa ndiye kuti ndatetezedwa kwa miyezi isanu ndi umodzi,” anatero a James.
Iwo apempha makolo anzawo kuti asazenegereze koma kuti atengane ndi kukalandira katemerayo.
“Chinanso chofunikira ndi kulimbikitsa ukhondo m’makomo mwathumo. Tikhale ndi zimbudzi zosamalidwa bwino, tizimwa madzi aukhondo komanso kusamba m’manja tikachokera ku chimbudzi,” anatero a James.