Mkwaso

Mphunzitsi amangidwa chifukwa chogwilirira mwana

Apolisi ku Namwera m’boma la Mangochi amanga mphunzitsi wa pa sukulu ya pulaimale ya Luchichi, a William Songolo a zaka 27 chifukwa chogwilirira mwana wa sitandade 2 wa zaka zisanu ndi chimodzi (6).

Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, izi zinachitika pa 29 Januwale chaka chino, m’mudzi wa Chimwala, mfumu yaikulu Jalasi.

A Daudi ati woganiziridwayu, yemwe amagwira ntchito ndi abambo ake a mwanayu, wakhala akumuphunzitsa mwanayu maphunziro a padera (part-time).

Nkhaniyi ikuti pa tsiku lomwe izi zidachitika, abambo ake a mwanayo, omwe anali ali ku sukulu kophunzitsa, analandira foni kuchokera kwa akazi awo kuwauza kuti abwerere kunyumba mwansanga chifukwa panali nkhani yokhudza mwana wawo.

“Atafika kunyumba, abambowo anaona zinthu zoyera ku maliseche a mwanayu, zomwe zimaganiziridwa kuti ndi umuna (semen).

“Atamufunsa mwanayu, iye anaulula kuti atamaliza kuphunzira, aphunzitsi ake anamunamiza kuti akukamugulira chinangwa, komwe anamutengera pa tchire lina,” atero a Daudi.

Iwo ati woganiziridwayu anamuuza mwanayo kuti achotse zovala zake, kenako anagona naye. Mwanayu anabwerera kwawo cha m’ma 4 koloko madzulo ndipo patadutsa nthawi anayamba kudandaula za ululu ochokera ku maliseche kwake, zomwe zinadabwitsa amayi ake.

Malingana ndi a Daudi, woganiziridwayu amachokera m’mudzi wa Kadaona, mfumu yaikulu Mzikubola, m’boma la Mzimba.