Osamamvera chisoni anthu a ulumali
Bungwe loyang’anira mabungwe ogwira ntchito za anthu a ulumali mdziko muno la Federation of Disability Organizations in Malawi (FEDOMA) lapempha anthu kuti asamamvere chisoni munthu wa ulumali chifukwa zimalimbikitsa ulesi.
Wamkulu woyendetsa ntchito ku FEDOMA a Ethel Kachala ati anthu akamamvera chisoni munthu wa ulumali, izi zimachititsa anthuwa kukhala osatakataka chifukwa amachirandira chisoni chija ngati kuti momwe moyo ukumayenera kukhalira.
“Chisoni chikawonjeza chimachotsa kulimba mtima, nde munthu wa ulumali akamamveredwa chisoni kwambiri nayenso amayanba kuchilandira chisoni chija ndikumawona ngati moyo ndiwomangomveredwa chisoniwo. Choncho ndikumalephera kutengapo mbali pa ntchito za chitukuko komanso zodzitukula ndipo amngodikirira kwa anthu ena,” natero a Kachala.
Iwo amalankhula izi Lachinayi pa mapeto pa mkumano wopereka upangiri kwa adindo ena m’boma la Balaka pa momwe angamagwirire bwino ntchito ndi anthu aulumali.
A Kachala anati chisoni sichofunika kwa munthu wa ulumali ndipo m’malo mwake anthuwa amafunikira kupatsidwa thandizo lokwanira kuti athe kupanga zinthu payekha popanda kudalira ena.
Malingana ndi ambiri omwe anatenga nawo mbali pa mkumanowo, zokambiranazo zinawatsegula m’maso kwambiri pa nkhani zosiyanasiyana za anthu aulumali.
A Trevor Dambe womwe anayimira wamkulu woyang’anira ntchito za mapulani ndi chitukuko m’bomali anapempha nthumwizo kuti zikagawne ndi ena zomwe anaphunzira ku mkumanowu ndicholinga chopititsa patsogolo umoyo wa anthu a ulumali.