MkwasoUncategorized

Rafik Mussa wapita ku Masters

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Katswiri wakale wosewera pakati ku timu ya Mighty Be Forward Rafik Mussa wasaina kontilakiti ya zaka ziwiri ku timu ya Masters Security FC komwe akhaleko mpaka chaka cha 2020.

Masters ikuonjezera mphamvu ku timu yake pokonzekera mpi- kisano wa chikho cha Confederation of African Football (Caf) pomwe ikukumana ndi timu ya Petro de Lu- anda ya ku Angola.

Mussa, wakhala asakupeza mpata wosewera ku timu ya Wanderers mu sizoni yangothayi. Iye wayamba kale kuchita mapulakatesi ndi timu ya Masters.

Pamene timasindikiza nyuzi- pepalayi wosewerayu samapezeka pa lamya wake koma munthu yemwe amakhala naye pafupi ana- tsimikiza kuti Mussa wasaina konti- rakiti.

“Ndizoona kuti wasaina konti- rakiti ya zaka ziwiri ndipo walandira kale K3 miliyoni yomwe wosewera amapatsidwa akamasaina. Koma mufunse zambiri ku timuyo,” anatero munthuyo, yemwe anati asatchulidwe dzina.

Mlembi wamkulu wa Masters, Zacharia Nyirenda, sanakane kapena kuvomera za nkhaniyi tita- mufunsa.

“Sindinganene kanthu za nkhaniyi mpaka pa 31 January,” anatero Nyirenda, popanda kunena

chifukwa chomwe sanganenere zambiri pano.

Koma mmodzi mwa akuluakulu ena a Masters FC, anatsina khutu Mkwaso kuti wosewerayo wasainadi kontirakiti ndi timuyi.

“Nditha kutsimikiza kuti Rafik ali mu banja lathu la Masters. Anayamba kale kuchitanso mapu- lakatesi. Analandira ndalama yake yosainira,” anatero.

Kontirakiti yake ndi Wanderers inayenera kutha chaka cha mawa koma Mussa ati wapempha kuchoka ku timuyi kuti adzikapeza mwayi wosewera.

Masters FC yasainanso wose- wera wakale wa Moyale Barracks, Fred Limbani.