MkwasoUncategorized

‘Tisasiye kupemphera kaamba ka matenda a coronavirus’

Wolemba: Alfonso MPIMA, Mtolankhani Wapadera

Episkopi wa Dayosizi ya Zomba ya Mpingo wa Katolika Ambuye George Tambala apempha akhristu kuti asasiye kupemphera kaamba ka matenda a coronavirus koma m’malo mwake azamitse mapemphero awo kuti madotolo apeze mankhwala kapena katemera wothana ndi matendawa.

Ambuye Tambala amalankhula izi m’dayosiziyo potsatira kulankhula kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika kuti anthu asamasonkhane oposa 100 malo amodzi ngati mbali imodzi yopewa matendawa.

Tambala: Musataye chikhulupiriro

Malinga ndi Episkopiyu, Mpingo upitiriza kumvera zomwe boma lapempha mzika za dziko lino zomwenso zambiri mwa izo ndi akhristu, potsatira njira zofuna kuthana ndi mliri wa corona.

“Ife ngati Mpingo tikhala tikudikira achipatala kuti afotokozanji zokhudza nthawi yoyenera kuti tiyambenso kumasonkhana limodzi ndi kumapemphera mwa nthawi zonse.

Ndipemphe akhristu kuti asataye chikhulupiriro chifukwa Mulungu ali nafe. Iyi ndi nthawi yoti tilumikizane m’mabanja, komanso kudzera pa wailesi za Mpingowu ndikumapemphera kuti nthendayi isafale komanso ithe pa dziko lapansi. Chikalata chomwe tatulutsa sitinanene kuti anthu asiye kupemphera ayi koma achilimikebe” anatero Ambuye Tambala.

Iwo ati matenda a Corona akhudza mayiko ambiri ndipo n’kofunika kusamala pozindikira kuti kupewa kumaposa kuchiza ndipo ati pakufunika kuti anthu asadikire kuti matendawa afike koma ayambiretu kupewa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *