MkwasoUncategorized

Waxy Kakufuna msika wakunja

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Waxy K, yemwe adaimba nyimbo ya ‘Za Zii’ wati tsopano akufuna ayambe kuimba nyimbo zimene zizikondedwa ngakhale ku maiko akunja.

Woimba wachisodzerayu wati ndiwokondwa ndi momwe anthu amulandilira m’dziko muno koma wati mtima wake udzakhazikika nyi- mbo zake zikayamba kukondedwa ndi anthu a maiko ena.

“Ndine wokhutira kwambiri ndimmene anthu akudzikondera nyi- mbo zanga,” anatero Waxy K.

“Sindimayembekezera kuti nyi- mbo zanga zingatchuke mmene zatchukiramu. Koma malingaliro anga ndioti tsopano ngakhale anthu amaiko ena azidzikonda.”

Waxy K, yemwe ndi mwana wa abusa, wati ayesetsa kumaimba nyi- mbo zongopereka malangizo.

“Makolo anga amandilangiza kuti ndizikhala wa makhalidwe abwino ndipo ndimayesetsa kutero.”

Waxy K, yemwe nyimbo yakenso ya ‘My Foot’ yatchuka kwambiri waulula kuti akufuna kutolera nyimbo zake zonse ndikupanga chimbale chi- modzi. Iye wati mutu wa chimbale chimenechi ukhala ‘Usalire’.

Rab Processors ikufuna chiphadzuwa

Wolemba:
Florence CHILANGA

Kampani ya Rab Processors yati ili kalikiliki kupangitsa mpikisano wo- funa kupeza chiphadzuwa chimene chikuyembekezeka kumadzaikidwa pa sopo wawo wotchedwa diva.

Kampaniyi imapanga zinthu monga ufa, masamba a tiyi, sitoko mwa zina. M’ modzi mwa akulu- akulu oyendetsa mpikisanowu umene akuutcha Diva Fame Photo- genic Seggoh Mndeme wati chiphadzuwa chimene chikufunika- cho akuyang’ anira kwambiri nkhope ya munthu.

“Tingoyang’anira kuti amase- kerera bwanji, amaoneka bwanji pa zithunzi ndi zina zokhudza nkhope basi. Tikufuna munthu ameneyu tidzimuika pa sopo wathu wa Diva,” anatero Mndeme.

Iwo anatinso amene ali oyenera kulowa mpikisanowu ndi atsikana amene a zaka zoyambira 18. Mpi- kisanowu uchitika pa miyezi isanu ndi umodzi (6) ndipo ndalama yolowera mpikisanowu ndi K5,000.

“Tsiku lomaliza kulembetsa ndi pa 18 January 2018, tidzajambula kuyambira pa 15 January ndipo ku- vota koyamba kudzakhala pa 30 Jan- uary 2018 Sitidzalola kudzikongoletsa nkhope kwambiri mu mpikisanowu,” anatsindika Mndeme.

Mndeme anati anthu azidza- votera munthu amene akufuna kuti achoke kufikira adzatsale m’ modzi. Iwo ati wopambana adzalandira ndalama zokwana K300,000.

“Tikudziwa kuti pakhala zovuta ndithu chifukwa aka ndi koyamba. Komabe ndi nthawi, tili ndi chikhulupiriro kuti zinthu zizikhala zikusintha,” anatero Mndeme.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *