News

YAS ipempha Amalawi kulondoloza malipoti a chuma cha boma

Bungwe la Youth and Society (YAS) lapempha Amalawi kuti adzikhala ndi chidwi cholondoloza ndi kuzukuta malipoti omwe ofesi ya wamkulu wolondoloza chuma cha boma (Auditor General) imatulutsa ngati njira imodzi yowonetsetsa kuti chuma cha boma chikugwiritsidwa bwino ntchito.

Wamkulu wa bungweli a Charles Kajoloweka ndiwomwe analankhula izi pa maphunziro apadera a atolankhani pa nkhani ya kalondolozedwe ka ndalama za boma ndi udindo wawo mu mzinda wa Lilongwe posachedwapa. Iwo anati izi zitha kuthandizira kuti akuluakulu a m’maofesi komanso nthambi za boma asatayilire pa kagwiritsidwe ntchito ka chuma cha boma.

“Anthu ambiri sakumakhala ndi chidwi kulondoloza kuti mu malipotiwa muli chani komanso kuti malipotiwa apeza chani cholakwika, izi ndizosayenera chifukwa potero zikungowonetsa kuti boma likungotaya ndalama ndi nthawi pomapanga kafukufuku ameneyu,” anatero a Kajoloweka.

Iwo anatinso ndizodandaulitsa kuti kwa nthawi yayitali malipotiwa akatuluka nthambi zina sizimachitaponso kanthu monga kuzenga milandu anthu omwe atchulidwa m’malipotimo.

“Awa ndi malipoti ofunikira kwambiri pogwiritsa ntchito yowonesetsa kuti adindo omwe akusakaza chuma cha boma akuzengedwa milandu. Choncho ndizodandaulitsa kuti kwa nthawi yayitali malipotiwa samagwiritsidwa ntchito ndi adindo kapena nthambi zosiyanasiyana ngakhale mutapezeka zofooka. Izi zikumawonetsa ngati kuti malipotiwa ndiwopanda ntchito,” iwo anatero.

Polankhulaponso pa maphunzirowo womwe anali mbali imodzi ya ntchito yothana ndi katangale ya bungwe la YAS yomwe ikuthandizidwa ndi bungwe la UNDP, mmodzi mwa akuluakulu ku ofesi yolondoloza chuma cha boma ya National Audit Office (NAO) a Jika Mapila, iwo anati ndikofunikira kwambiri kuti atolankhani azizukuta malipotiwa chifukwa zimathandizira kubweretsa poyera zofooka zomwe maofesi ndi nthambi za boma amachita pa nkhani ya chuma.

Wolemba Precious Msosa

#MontfortMedia