Uncategorized

ZENIZENI NZITI ?

Wolemba: Joseph kayira.

Pamene nkhawa yakula pa zakatemera wa Covid-19 wa   AstraZeneca, yemwe boma lanena kale kuti akhala akufika m’dziko muno masiku ochepa akudzawa, anthu akuti boma likanayamba laima ndi kudikira kuti lionetsetse ngati katemerayu ngodalirika. Koma pulezidenti wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi nduna yofalitsa nkhani, yomwenso ndi mneneri wa boma, a Gospel Kazako anenetsa kuti boma laitanitsabe katemerayo pofuna kuthandiza anthu ndi kuchepetsa kufala kwa matendawa.

Malingana ndi malipoti, pali kampani zosiyanasiyana zomwe zapanga katemera wokwana m’sanu ndi mutatu (8), monga ya Pfizer BioNTech ndi Moderna, koma dziko la Malawi lasankha katemera wa AstraZeneca yemwe wapangidwa ku Oxford ku Mangalande mogwirizana ndi akatswiri amu dziko la Sweden, yemwe akuti kusamala kwake nkosavuta pofanizira wa kampani zinazo yemwe amasowa malo ozizira kwambiri a pakati pa madigiri 2 ndi 8 kuti asungidwe bwino. akatemera enawo amafunika malo ozizira kuposera apa zomwe ndizovuta kukwaniritsa m’maiko ambiri a kunsi kwa chipululu cha Sahara.

Malingana ndi kafukufuku, munthu akabaidwa katemerayu, amathandiza kuonjezera mphamvu ya m’thupi yolimbana ndi tizilombo ta Covid-19. Koma pali nkhawa tsopano patamveka kuti ngakhale kuti anthu akubaidwa katemerayu, ena akupezekabe ndi tizirombo ta Covid-19. Polankhula ku mtundu wa Malawi, Pulezidenti Chakwera wati anthu asade nkhawa ndi manong’onong’o pa za katemerayu chifukwa katemerayu ali ndi kuthekera koteteza anthu ku mliri wa Covid-19 kupyola theka (50 peresenti).

Koma maiko monga South Africa, komwe matendawa avuta kwambiri kuposa kwina kulikonse muno mu Africa, katemera wa AstraZeneca, waimitsidwa kaye ati kaamba koti pali chikaiko ngati  angachiritsedi matendawa — maka omwe abuka kumene omwe akusiyana ndi Covid-19 woyamba uja. Koma a Chakwera ati katemerayu ndi wovomerezeka ndi bungwe la World Health Organization (WHO), European Medicines Agency (EMA) komanso Food and Drug Administration. Iwo ati dziko la Malawi lipitirira kuunikira zomwe zikuchitika pa kafukufuku wa katemera kuti lithe kupeza katemera amene angakhale woyenera kwenikweni ku dziko la Malawi.

“Koma ndimafuna ndipemphe anthu kuti poganizira nthawi imene katemerayu angatenge kuti ayambe kuperekedwa kwa anthu, ndalama zomwe zikufunika komanso zina zosamwitsa zokhuza chikhalidwe chathu, chida chabwino kwambiri polimbana ndi matenda a Covid-19 ndi kuziteteza,” a Chakwera atero. Pali nkhawa yoti katemerayu sanatenge nthawi yaitali kuti afufuzidwe ndipo izi mwina zikhoza kupereka chiopsezo pa umoyo wa munthu amene angalandire katemera.

Ena akuti katemerayu akhoza kupereka chiopsezo chachikulu pa moyo wa munthu chifukwa sanamufotokozere bwino momwe akugwirira ntchito nkuona maiko ena akumukana. Koma bungwe la WHO ndi boma akuti palibe choopsa chilichonse ndi katemerayu. Nduna yofalitsa nkhani a Kazako akuti “boma silingatenge ziphe nkubweretsa kuno ku Malawi ncholinga chodzapereka kwa anthu.”

“Katemera aliyense amabwera ndi zake, uyunso sitikudabwa kuti wabwera ndi manong’onong’o. Kunali katemera wa nthomba ndi wina yemwe anthu alandirapo m’mbuyomu ndipo anagwira bwino ntchito mmatupi a anthu. Uyunso tikukhulupirira kuti ndi wabwinobwino.

Amene akukana kulandira katemerayu akuika moyo wawo pa chiswe. Boma silikukakamiza munthu kulandira katemerayu,” atero a Kazako.

Nayo nduna ya zaumoyo a Khumbize Chiponda yati katemera amene lasankha dziko lino wa AstraZeneca athandiza kuchepetsa kufala kwa matendawa ndipo kuti chitetezo chimene katemerayu akupereka chapakati pa maperesenti   opyola 50 chikupereka chiyembekezo kuti anthu atha kuthandizika.

“Tipitirira ndi dongosolo loitanitsa katemerayu. Chofunikira ndi choti katemerayu achepetsa zizi-ndikiro komanso zowawa zomwe anthu amakumana nazo pa matenda a Covid-19. Ena akunena za akatemera osiyanasiyana kuti amapereka chitetezo chokwera koma chomwe ife tikudziwa ndi choti akatemera enawa akufufuzidwabe ndi kukonzedwabe. “Tikukambirana ndi a WHO kuti tiyende bwanji pa nkhaniyi,” anatero a Chiponda.

Malingana ndi chikaiko chimene chilipo pa katemerayu ena akuti nkofunika kuti andale monga pulezidenti, nduna, atsogoleri a zipani ndi akuluakulu a m’boma adzakale oyambirira kulandira katemerayu kuti anthu atsimikizedi kuti si ziphe.

Bungwe la Malawi Health  Equity Network lidauza nyuzipepala ya The Nation ya Lachiwiri pa 9 Febuluwale kuti ndi lokhumudwa ndi momwe nkhani yakatemera iku­­­­­­mvekera kaamba koti anthu sakudziwa choona chenicheni cha katemera wa Covid-19.

Mkulu wa bungweli a George Jobe anati ndizokhumudwitsa kuti pali zambiri zomwe zikukambidwa pa katemera ndipo ena nkhaniyi ailowetsa ku chipembedzo. A Jobe akuti nkofunika kwambiri kuti boma lilimbikitse nkhani yophunzitsa anthu za katemerayu ndipo chifukwa zambiri zomwe anthu akuuzidwa ndi zosalondola.

“Ife tikugwira ntchito ndi boma ndipo tikudziwa kuti pali akatswiri ambiri amene akutumikira poonetsetsa kuti zinthu ziyende bwino pa            katemerayu. Sindikukhupirira kuti boma lingabweretse katemera woipa kwa Amalawi. Katemera aliyense amakhala ndi ubwino ndi kuipa kwake. Izi ndi zomwe tikufuna kuti anthu afotokozeredwe,” atero a Jobe.

Ena mwa maiko amene akhala akukana za katemera wa Covid-19 ndi Madagascar ndi Tanzania. Maikowa akhala akugwiritsa njira zawo polimbana ndi matendawa osati zomwe a WHO anauza maiko. Boma liri pa ntchito yaikulu yodziwitsa anthu zenizeni za katemnera wa AstraZeneco kaamba koti mbiri ya katemerayu yaipa kudzera mwa anthu amene akuti katemerayu siwabwino. Koma m’maiko ambiri ku Ulaya anthu ayamba kale kulandira katemerayu.