2025 chinali chaka choliritsa
Wolemba: Joseph KAYIRA
Ngakhale chaka cha 2025 chikutengedwa ndi anthu ambiri kuti chinali chaka cha masautso, anthu ena akuti palinso zina zabwino zomwe zaika dziko la Malawi pa mapu – monga kuye-ndetsa bwino kwa chisankho chachikulu ndi bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) – pamene m’maiko ena omwe taya-ndikana nawo, zisankho zoterezi zinathera m’ziwawa.
Pa chisankhocho, mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP), a Peter Mutharika, anago-njetsa yemwe anali mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwera, a Malawi Congress Party (MCP), nkubwereranso m’boma. A Mu-tharika adagonja kwa a Chakwera pa chisankho chomwe chinachitikanso m’chaka cha 2020, khoti lapadera litagamula kuti chisankho cha mu 2019 chinali ndi zolakwika zambiri.
Kadaulo pa nkhani za ndale – yemwenso ndi mphunzitsi pa phu-nziro la ndale ku sukulu yaukache-njede ya Univesite ya Malawi – a Joseph Chunga – afotokozera nyuzipepala ya Mkwaso kuti kuye-ndetsedwa bwino kwa chisankho chachikulu pa 16 Seputembala chaka chino kunapereka chiye-mbekezo kuti demokalase iku-khwima komanso kuti mwina Amalawi awona kusintha.
Iwo ati ngakhale kuti Amalawi anapanikizika m’chakachi ndi ma-vuto odza kaamba kakusokonekera kwa ntchito zachuma – itafika nthawi ya chisankho, zinthu zinayenda mwadongosolo ndipo panalibe ziwawa “mwa zina kaamba koti mtsogoleri amene amalamulira nthawiyo, anavomereza msanga zotsatira za chisankho cha pulezidenti.”
“Ngakhale panali ena amene amakaikira bungwe la MEC, makamaka kumayambiriro a zokonzekera za chisankho, tinaona kuti bungweli linayendetsa chisankho mwau-kadaulo. Pa zisankho za m’mbu-yomu – monga m’chaka cha 2014, 2019, kudzanso 2020 – sikunali kwapafupi kuti olephera pa chisankho cha pulezidenti avo-mereze zotsatira.
“Zinangovuta kuti nthawi imene timayembekezera kuti atsogoreliwa asinthane mphamvu, mtsogoleri wakale [a Chakwera] sanakwanitse kukhala nawo pa mwambowo. Vuto ndi loti panali kusamvana pakati pa mbali ziwiri zimene zinkayendetsa mwambowo. Kunangoyenera kuti mtsogoleri wopambana [a Mu-tharika] awalangize anthu ake kuti apewe kulankhula mokhadzula koma momanga ndikubweretsa umodzi,” anatero a Chunga.

Nkhani ya kusowa kwa mafuta a galimoto inasautsa kwambiri chaka chatha (Photo Credit: The Chord Tv)
Iwo anafotokozanso kuti Ama-lawi ambiri anataya chikhulupiriro mwa atsogoleri a boma lapita lija kaamba koti ntchito zachuma zinali zitasokonekera kwambiri. A Chunga anafotokoza kuti kusokonekera kwa ntchito zachuma kunapsinja anthu ambiri, ndipo izi ndi zina mwa zomwe zinachititsa kuti anthuwa aganize zosintha utsogoleri.
Katswiriyu anati kafukufuku amene mabungwe, monga Afrobarometer ndi ena, akhala akuchitika m’mbuyomu anapeza kuti Amalawi ambiri samaona tsogolo lowala m’chakachi kaamba ka mavuto a zachuma komanso kusakhutira ndi utsogoleri wa nthawiyo.
“Muona kuti kunali vuto la kusowa kwa ndalama zakunja, vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto, kuthimathima kwa magetsi komanso kusowa kwa chakudya. Zonsezi zinabweretsa ululu kwa-ambiri pakati pa Amalawi. Tili pa nkhani ya chakudya muona kuti chaka chilichonse timakhala tikudandaula za njala mpaka kumagula chimanga ku Zambia, monga m’mene zakhalira chaka chino, zomwe pena zikuongoonetseratu kulephera kwathu pa ntchito yotumukira bwino komanso pothana ndi vuto la njala.
“Kwa zaka zambiri timada-ndaula ndi njala kapena kuchepa kwa chakudya. Funso ndi loti ndi chani chimene anzathu akukwa-nitsa kuchita chimene ife kuno ku Malawi sitikukwanitsa? Komanso chakudya sichimanga chokha. Kusowa kwa chimanga kutipatse nzeru kuti tiike ndondo-meko zovomerezeka komanso zothandiza kuti tizitha kukhala ndi chakudya chokwanira kuti Amalawi asapitirire kumapsi-njika chaka chilichonse,” anatero a Chunga.
Malingana ndi malipoti, Amalawi pafupifupi 4 miliyoni akufunika thandizo la chakudya la msanga-msanga. Boma laitanitsa chimanga chokwana matani 200,000 kuchokera ku Zambia kuti lithandize anthu amene akusowa pogwira. Pali ma-ntha oti chiwerengero cha anthu amene akufunika thandizo la cha-kudya chithanso kukwera – maka miyezi ya pakati pa Januwale ndi Malichi pomwe njala imafika pachimake kuno ku Malawi.
A Chunga afotokoza kuti nkofunika tsopano kuti, Malawi ndi maiko ena amu Africa, ayambe kukambirana mozama za momwe angatumikire bwino anthu awo. Iwo ati kutumikira bwinoku kukufunika pa nkhani za chuma, chitukuko, ulimi komanso ulamuliro wabwino, mwa zina.
“Kupita chitsogolo, tilingalire mwakuya momwe tingaimire patokha pa chuma posadalira mabu-ngwe monga International Monetary Fund (IMF), World Bank ndi ena. Tikhale ndi masomphenya. Mwa zina, tiike mmaudindo anthu oyene-rera osati chifukwa cha ndale koma chifukwa choti ndioyenerera kukhala m’maudindowo.
“Chaka cha 2025 chakhala chosautsa, monganso zimakhalira m’mbuyomu, chifukwa kunali kulekerera katangale. Kuthana ndi katangale sikukusowa anthu aku IMF kubwera nkudzatiuza kuti izi ndizolakwika. Ku China amakwanitsa kuthana ndi amene akuchita ktangale kapena kusakaza chuma cha boma chifukwa anakhazikitsa malamulo okhwima,” anatero a Chunga.

Chunga: Tikuyenera kusintha kachitidwe ka zinthu (Photo Credit: Internet)
Mkuluyu wati Amalawi asa-makhalire kudandaula – mwa chitsanzo – maiko akunja, monga m’mene linachitira dziko la United States – akasiya kuthandiza dziko lino. Iwo anati nthawi yakwana yoika mfundo zogwirika pofuna kutukula Malawi osati kudalira maiko otukuka.
“Tiime patokha pa chuma ngati tikufuna kutukuka. Maiko akasiya kutithandiza tichitenge ngati mwai wapadera wounikanso m’mene timachitira zinthu. Mwa chitsanzo, dziko la America litasiya kutithandiza tinayenera kupeza mfundo zabwino zoti tipite chitsogolo.
Tisachedwe ndi kulira ndi kumafunsa mafunso kuti dziko la America lasiyiranji kutithandiza. Mtsogoleri wa dziko la America, Pulezidenti Donald Trump akupanga zoyendetsa dziko lake; nafenso tipeze njira zoti tipulumukire,” anatero a Chunga.
Kaamba kakusokonekera kwa ntchito zachuma, Amalawi ambiri anakhuzidwa m’chaka cha 2025 ndipo umoyo wawo unali wolimba. Ntchito za bizinesi zinasokoneke-ranso ndipo makampani ena ana-kakamizidwa kuchotsa ntchito anthu awo kaamba kosakwanitsa kupanga phindu. Kugwa kwa ndalama ya kwacha mu chaka cha 2024, kunapangitsanso kuti zinthu zisoko-nekere kwambiri pa chuma m’chakachi.
Akatswiri pa ndale ndi pa chuma akuti kuyenda bwino kwa chisankho chachikulu ndi mtendere umene dziko la Malawi liri nawo, ku-ngathandize kuti ntchito zachuma ziyambe kubwerera mchimake. Koma iwo achenjezanso kuti boma latso-pano likuyenera kuthana ndi kata-ngale ngati poyambira kumanga Malawi watsopano.
