Madzi aku Mpira Damu siamudzi umodzi – Nyirenda

Nyirenda: Tikuyesetsa kuti anthu akhale ndi madzi

Wolemba: Joseph KAYIRA

Kwa anthu okhala ku Balaka ndi ku Ntcheu omwe amadalira madzi ochokera ku damu la Mpira, akhala akukumana ndi vuto la madzi kwa zaka zambiri. M’chaka cha 2018 damuli lomwe liri m’boma la Ntcheu linaphwera ndipo vuto lakusowa kwa madzi linafika povutitsitsa. A Onances Nyirenda, omwe ndi mkulu woona za madzi m’boma la Ntcheu akuunikira za mbiri ya Mpira Damu komanso zina zomwe zachititsa kuti ntchito ya Mpira-Balaka Rural Piped Water Project ikumane ndi zokhoma popereka madzi kwa anthu a m’maboma awiriwa ndi madera ozungulira. Mkwaso unacheza ndi a Nyirenda motere:

Kodi damu la Mpira linamangidwa liti ndipo chinachititsa kuti limangidwe ndi chani?

Damu la Mpira linamangidwa kuyambira m’chaka cha 1987 kufika 1988. Damuli linamangidwa kuti lizitha kusunga madzi ochuluka kwambiri ndipo limaperekera madzi m’dera la makilomita 42.3 mlitali komanso mlifupi. Kumangidwa kwa damuli kunadza pofuna kuthana ndi mavuto a madzi kwa anthu okhala ku Balaka ndi madera ozungulira. Panali mavuto monga okhuza chilengedwe, chuma ndi ena kumunsi kwa damuli. Dziwani kuti boma la Balaka liri m’dera lovuta madzi.

Pali mapaipi olukanalukana otalika mlingo wa makilomita 1,600. Ndipo sikimu ya madzi ya Mpira ili ndi matapu omwe anthu amatungapo m’magulu oposa 2,000 komanso pali malo oposa 600 omwe alumikizidwa ngati nyumba kapena ofesi penanso bizinesi. Tili ndi malo atatu komwe madzi amagaidwa kapena kuti amakonzedwa kuchotsa zinyalala, mchenga ndi zina zotero. Sikimu ya madzi ya Mpira ili ndi mathanki 42 osungiramo madzi. 

Ndalama zomangira damuli zinachokera kuti?

Ndalama zomangira damuli zinachokera ku African Development Bank, yomwe inali ngogole, Danish International Development Agency, omwe anangothandiza, komanso zina zinachokera ku boma la Malawi.

Panthawiyo ndi anthu angati omwe amayenera kulandira madzi kuchokera ku damuli? Nanga ndi angati omwe akumwa madzi ochokera ku Mpira pakali pano?

Madzi ochokera ku Mpira Damu amafikira anthu pa mtunda wa 1,900 mlitali ndi mlifupi m’maboma a Balaka, Ntcheu, Mangochi ndi Neno. Pachiyambipo, mapulani anali ofikira anthu 354,000 koma pano ndi anthu oposa 515,000 omwe akumwa madziwa. Kwa amene ali mtauni ya Balaka, a Southern Region Water Board akutengapo mbali yogawa madzi kwa anthuwa.

Mbali imodzi ya damu la Mpira

Anthu ena omwe tacheza nawo akudandaula za kuvuta kwa madzi; ena anasiya kulandira madzi zaka khumi kapena kuposera apo. Chikuchititsa izi ndi chani?

Pali zambiri zomwe zikuchititsa kuti madzi azivuta – zina ndi zokhuza ku ofesi zinanso momwe anthu akuchitira mbali inayi. Mwa chitsanzo, zokhuzana ndi momwe anthu akuchitira ndi kuonongeka kwa chilengedwe kaamba kodula mitengo mwachisawawa komanso kuotcha makala. Izi zachititsa kuti mu damuli muzipezeka matope ndikuchititsa kuti ntchito yokonza madzi asanafike kwa anthu izidya ndalama zambiri.

Kuba kwa zipangizo monga mapaipi, kwasokonezanso kwambiri ntchitoyi. Matope omwe ali mu damuli pena amatseka mapaipi akuluakulu omwe amatenga madzi kupititsa kwa anthu zomwe zimachititsa kuti anthu asalandire madzi. China ndi choti sikumuyi yakhalitsa komanso  inakonzedwa kuti izipereka madzi kwa anthu 354,000 koma pano chiwe-rengerochi chakwera kawiri.

Palinso mavuto monga kuti anthu sanazindikiritsidwe bwino za momwe sikimu ya madziyi imayendera. Pali anthu ena omwe safuna kulipira madzi; amafuna azimwa aulere. Awa ndi omwe amaona ngati madziwa akuyenera kuperekedwa kwa aliyense mwaulere kuiwala kuti pamafunika ndalama kuti madziwa aperekedwe kwa aliyense.

Nthawi zinanso ndale zimalowererapo pa ntchitoyi. Chinanso ndi choti ndalama sizimatoleredwa bwino komanso mosakwanira. Izi zimakhuza ntchito yoperekera madzi kwambiri. Komanso tinene pano kuti anthu ofuna madzi achuluka kwambiri ndipo tikayerekeza ndi mapulani oyambirira aja sizikugwira.

Ndiye anthu mukuwauza motani kuti amvetse za mavutowa komanso mukuchitapo chani kuti madzi afikirebe anthu?

Pakali pano boma lapereka ntchito yoyang’anira madzi kwa anthu kudzera mu Water Users Association (WUA) – pansi pa Mpira Water Trust. Choncho dongosololi likupereka mphamvu yoyang’anira ndi kukonza zomwe zingaonongeke monga mapaipi ndi zina kwa anthu eni ake koma mothandizana ndi wamkulu wa sikimuyi mothandizidwa ndi Ofesi yoyang’anira madzi pa boma.

Zikuoneka kuti komwe kumachokera madzi olowa mu damuli kwasokonezedwa chifukwa chodula  mitengo mwachisawawa, kuotcha makala komanso ulimi wosatsatira ndondomeko zovomerezeka. Mukuchitapo chani kuti muonetsete kuti damuli lisaphwerenso ngati mmene zinalili zaka zingapo zapitazo?

Unduna wa za madzi wathandizapo pa kafukufuku wofuna kupeza ndondomeko zowonetsetsa kuti madzi akupezeka nthawi zonse ndipo zotsatira zake zatuluka. Athandiza ndi ndalama za kafukufukuyu ndi a International Development Agency (IDA-World Bank Group) ndipo thandizoli ndi mbali imodzi yothandiziranso mbali yoyamba ku ntchito ya Shire River Basin Management Programme.

Lipotili lithandiza kuti pamangidwe zinthu zoyenerera kuti vuto lamadzi lithe; kuti madzi azipezeka chaka chonse kwa anthu akumudzi, posaononga chile-ngedwe komanso kuti anthu azitha kukhala ndi chuma chokwanira pa miyoyo yawo ya tsiku ndi tsiku. Pali maganizo okonzanso sikimu ya Mpira-Balaka Rural Gravity-fed Piped Water Supply yomwe monga ndanena yili mmaboma a Ntcheu, Balaka komanso mbali zina za maboma a Neno ndi Mangochi.

Mumafunika madzi ochuluka bwanji kuti mupereke kwa anthu mopanda kudukiza?

Pamafunikatu madzi osachepera makyubiki (cubic) mita (metres) 18,540 pa tsiku.

Mwayeserako kuchotsa matope amene ali mu damuli kuti madzi azipezeka mosavuta?

Mapulani alipo okonzanso damuli kuti madzi akwere ndi mamita anayi (4). Palinso mapulani okonzanso nkhokwe ya madzi (reservoir) makilomita khumi (10) kuchokera ku Mpira Damu. Zonsezi cholinga chake ndi choti madzi azipezeka mosavuta chaka chonse.

Ndi chani china chimene mwachita poonetsetsa kuti madzi akupezeka kwa anthu omwe mumawatumikira?

Mjigo yakumbidwa m’midzi yosiyanasiyana kuti anthu akhale akumwa madzi abwino nthawi zonse.

Mipope yambiri idaononngeka

Anthu akumidzi ku Balaka akuti anavutika kwambiri kukumba migelo yomwe mwadutsa mapaipi. Iwo akuti ngakhale anavutika chonchi madzi awo akuperekedwa kwa okhala mtauni ya Balaka. Chenicheni nchiti pa nkhaniyi?

Choyamba ndi choti sikimuyi ina-yamba m’chaka cha 1988 mkutha mchaka cha 1992. Anthu amayenera kuchitapo kanthu pokukumba migelo yodutsa mapaipi. Nthawi imeneyo ndondomeko yonseyi inali pansi pa unduna wa madzi ndipo anthu samalipira kalikonse. Pano kayendetsedwe ka madziwa kasintha chifukwa kali m’manja mwa anthu.

Madziwa si a anthu akumidzi aku Balaka wokha ayi, koma a ku Ntcheu, Balaka ndi mbali zina za maboma a Neno ndi Mangochi, kuphatikizapo aku Balaka kutauni. Kukanakhala kuti malamulo amawalola a Mpira Dam Trust kuperekera madzi m’matauni bwenzi pano si a Southern Region Water Board amene amaperekera madzi mtauni ya Balaka.

Sizingachitire ubwino bomali kuti madziwa asamafike kutauni kaamba koti kumeneko ndi kumene kumachitika ntchito za chuma. Komanso dziwani kuti ndalama zimene anthu akutauni amapereka ndi zimene zimathandiza kuti ntchito yogawa madzi idziyendabe. Anthu asaone ngati a Trust akukonda ndalama poyerekeza ndi miyoyo ya anthu ayi. Dziwani kuti sikimuyi ikuyenda chifukwa cha ndalama zomwe zikuperekedwazi; popanda ndalama palibe chingayende.

Choncho ndi zoona kuti mwadula okhala ku midzi ndikumagulitsa madziwo ku Southern Region Water Board?

Zifukwa zimene anthu ena sakulandirira madzi ndadzitchula kale pamayambiriro paja. Ichi nchifukwa chake a Southern Region Water Board nawo akumba mijigo mmadera ena kuti azithandizira pomwe ochokera ku Mpira Damu akuvuta. Mukhoza kundi-vomereza kuti ngakhale mu tauni ya Balaka namo muli madera ena komwe madzi a m’mipope akuvuta ndithu.

Wina ndi ndani amene mukugwira naye ntchito yowonetsetsa kuti madzi sakuvuta kwa anthu amene mumawapatsa madzi?

Ndi unduna wa madzi umene uli ndi undindo wowonetsetsa kuti anthu ali ndi madzi aukhondo komanso okwa-nira; ina ndi ofesi yoona za madzi ku Ntcheu.