NCA-DCA yathandiza mabanja 750 ku Machinga
Wolemba: Joseph KAYIRA
Mgwirizano wa mabungwe a Norwegian ChurchAid ndi Dan ChurchAid (NCA-DCA), kudzera mu mgwirizano wawo ndi bungwe lomwe amagwira nalo ntchito mu mapulojekiti ena, la Find Your Feet – ndi thandizo la ndalama kuchokera ku bungwe la Danish International Development Agency (DANIDA) – athandiza mabanja 750 mu dera la Mfumu yaikulu – Paramaunti Kawinga – mu boma la Machinga omwe akhuzidwa ndi vuto la njala.
Tonde: Ndife okhuzidwa ndi malipoti a njala
Bungweli lagawa K80,000 kwa banja lirilonse kuti likwanitse kugula chakudya ndi zina zimene akuzisowa malingana ndi zofuna kapena zosowa za banja lirilonse.
M’modzi wa akuluakulu aku NCA-DCA, a Augustine Paul Tonde, ati iwo anali wokhuzidwa ndi malipoti oti anthu ambiri sanakolore chakudya chokwanira ndipo kuti mabanja ambiri akuvutika ndi njala m’deralo.
“Anthu ambiri kuno ku Machinga anakhuzidwa ndi zotsatira za El Nino, nyengo yomwe inachititsa kuti anthu asakolore bwino mbewu zawo. Mvula siinagwe bwino chifukwa cha nyengo ya El Nino. Choncho, ife tinachiona chinthu chofunikira kwambiri kuti tiwafikire anthuwa ndi thandizo la ndalama kuti agule chakudya ndi zosowa zina pa moyo wawo,” a Tonde anatero.
Mayi Kuyaka: Thandizo lafika mu nthawi yake
Iwo ati kudzera mu mgwirizano wawo ndi boma ndi mabungwe ena, anamva za ululu umene anthu a kwa Mfumu yaikulu Kawinga akukumana nawo ndipo anapeza ndalama zokwana K60 miliyoni kuchokera ku DANIDA kuti athandize kuchepetsa vuto la njalali.
“Ndikovuta kufikira aliyense koma ngati bungwe tachitako mbali imene takwanitsa. Ndi khumbo lathu kuti tithandize anthu ambiri amene akukumana ndi vutoli. Tikanakonda kuti pakhale njira zoyenerera pa nkhani yothana ndi njala kuti anthu azikhala ndi chakudya chokwanira,” anatero a Tonde.
A Patuma Afiki, a zaka 27, m’mudzi mwa Kamfosi, Mfumu yaikulu Kawinga, omwe analandira nawo thandizoli, anati ndiokondwa kuti a NCA-DCA awathandiza pa nkhani ya njala. Iwo akuti mvula siinabwere bwino chaka chino ndipo izi ndi zimene zachititsa kuti asakolore zokwanira.
“Kuno timadalira ulimi ndipo kusintha kwa nyengo kwatikhuza kwambiri chifukwa mvula siikubwera monga m’mene inkachitira kale. Anthu ambiri kuno alibe chakudya. Ana akumatha kukomoka ndi njala m’makomomu. Ndalama imene ndalandilayi indithandiza kuti ndikagule chakudya. Ndikuwathokoza amene atithandizawa chifukwa apulumutsa miyiyo,” anatero a Afiki.
Akuluakulu aku NCA-DCA kupereka ndalama
Iwo apemphanso anthu akufuna kwabwino kuti awathandize ndi zipangizo kuti ayeserenso ulimi.
“Fetereza wa makuponi sitinalandire; panopa tikumagula fetereza m’makapu woyeza uja. Tingathokoze anthu ena atabwera kuzatithandiza ndi zipangizo ngati mbewu ndi fetereza kuti tilime kuti tithane ndi njala chaka cha mawa,” anatero a Afiki.
Mayi Felina Kuyaka, a zaka 35 a m’mudzi mwa Chigunda, kwa Mfumu yaikulu Kawinga anati vuto la njala lakula kwambiri m’dera lawo ndipo thandizo la NCA-DCA labwera mu nthawi yake.
“Vuto la njala ndilalikulu kuno. Chakudya chikuchita kubwera kuchokera ku Mozambique. Anthu akukhalira kudya mango ndipo akangotha mangowa sitikudziwa kuti zitha bwanji. Ndikufuna ndiwathokoze mwapadera amene atithandizawa chifukwa atiphula pa moto. Enanso akufuna kwabwino abwere azatithandize chifukwa anthu amene akufunika thandizo la chakudya ndi ambiri,” anatero a Kuyaka, omwe ali ndi ana asanu.
Paramaunti Kawinga: Ndikuthokoza chifukwa cha thandizoli
Iwo anati m’madera ena anthu akusowa mtengo wogwira kaamba ka njalayi pano akudya chitedze. Mayiwa anati thandizo limene alandira likafikira anthu pamtundu pawo chifukwa akagula chimanga ndi kukachigawa akuti aliyense apezeko ka phala.
Mfumu yaikulu ya mtundu wa ayawo, Paramaunti Kawinga inati vuto la njala ndi lalikulu m’dera lake ndipo lakhuza anthu ambiri. Mfumuyi yayamikira a NCA-DCA chifukwa cha chifundo ndi chikondi chawo pogawa ndalama kwa anthu ake.
“Ndikuwapempha anthu, maka amayi, kuti ndalamayi siyopangira mkomya koma kuthandizira mabanja awo. Ndalamayi siyokagulira chitenge kapena mpango, koma akagulire chimanga kuti asafe ndi njala. Mwapadera ndikufuna kuwathokoza a NCA-DCA ndi DANIDA potiganizira kuno ku Machinga,” inatero Mfumu Kawinga.
Iyo yati mvula imene yakhala ikugwa mwa njomba ndi imene yapangitsa kuti mderalo mukhale njala. Kwa zaka tsopano, kusintha kwa nyengo komanso nyengo ya El Nino imene inapangitsa kuti mvula isagwe bwino chaka chatha, ndi imenenso yakolezera njalayo.
Mayi Afiki: Njala ili ponse ponse
“Munda umene ndimakolola matumba 120 chaka chino ndinangokolola matumba asanu ndi theka. Kunagwa mbozi zoononga komanso mvula inabwera mwa njomba. Anthu ambiri sanakolore bwino ndipo njala ilipo ndithu. Anthu amabwera tsiku ndi tsiku kwathu kuzapempha. Ndiwapemphenso ena akufuna kwabwino kuti athandizepo,” anatero a Kawinga.
Lipoti la Malawi Vulnerability Assessment Committee (MVAC), lomwe linatulutsidwa miyezi yapitayo, linati anthu oposa 4 miliyoni akhala akusowa chakudya pakati pa miyezi ya Meyi ndi Seputembala chaka chino. Akatswiri pa zaulimi akuti chiwerengerochi chikhoza kukwera pomafika chaka cha mawa, maka mu miyezi yomwe chakudya chimavuta ya pakati pa Januwale ndi Malichi.