NewsZa M'dziko

Gogo woganiziridwa ‘kumanga’ mvula apulumutsidwa

Apolisi m’boma la Balaka apulumutsa gogo wina yemwe amafuna kuchitidwa chipongwe poganiziridwa kuti ‘akumanga’ mvula m’mudzi wa Manjanja mfumu yayikulu Chanthunya m’bomali.Malingana ndi apolisi, mdzukulu wa gogoyu anawuza anthu pa 7 Januwale kuti agogo ake omwe ali ndi zaka 60 ndiwomwe akumanga mvula.Izi akuti zinakwiyitsa kwambiri anthuwa womwe anapanga upo wofuna kukachita chipongwe gogoyu.

Koma asanatero, apolisi anatsinidwa khutu ndikukamuthawitsa gogoyu ndikukamusunga ku polisi ya Balaka.Kutsatira izi, apolisiwa anakonza mkumano ndi anthu a m’mudziwu komwe wamkulu wa apolisi m’bomali a Dan Sauteni anakachenjeza anthu zakuwopsa kotengera lamulo m’manja mwawo.

Iwo anati ndizomvetsa chisoni kuti anthu akuganizabe kuti kuvuta kwa mvula ndichifukwa cha masalamusi a anthu.A Sauteni anati anthu akuyenera kuzindikira kuti kuvuta kwa mvula ndichifukwa cha kusintha kwa nyengo.Mfumu yayikulu Chanthunya inathokoza apolisiwa pobwera msanga kudzawombola gogoyu ndikudzawazindikiritsa.Pakadali pano, madera ambiri m’bomali sanayambe kulandira mvula molongosoka pomwe ikumangobwera yowaza.

Olemba Rose Chipumphula CHALIRA ndi Precious Msosa