MkwasoUncategorizedZa M'dziko

Ulimi ukusaukitsa dziko la Malawi – Kabambe

Wolemba: Yamikani PHIRI; Mtolankhani Wapadera

Gavanala wa banki yaikulu m’dziko muno ya Reserve a Dalitso Kabambe, ati dziko la Malawi likuyenera kuganiza mwamsanga njira zina zopezera chuma chifukwa ulimi ukulisaukitsa.

Malingana ndi a Kabambe zaka zoposa 50 zomwe zapita dziko lino likudalira ulimi chuma chake chakhala chisakusuntha. Iwo ati maiko omwe dziko la Malawi linkalingana nawo pa chuma zaka            zapitazo pano ndiolemera pomwe Malawi ali chisaukire.

Iwo amalankhula zimenezi pa msonkhano waukulu wa pachaka wa bungwe la Institute of Bankers in Malawi.

“Tisanene za maiko ena akutali ngati China, Korea koma akufupi ndi dziko lathu lomweli omwe sitimasiyana nawo kwambri koma pano ngolemera monga Kenya, yomwe m’chaka cha 1980 zopeza zake zinkaposa kanayi dziko la Malawi koma chaka chathachi cha 2018 zikuwonetsa kuti limaposa Malawi ndika 13”, anatero a Kabambe.

Sitingapitirire kukhala choncho- Kabambe

Iwo anati dziko lino liri ndi zinthu zambiri monga zokopa alendo, migodi ndi ntchito zina za mafakitale zomwe zikhoza kubweretsa chuma.

“Inu mukudziwa kuti ulimi womwe dziko lino lakhala likupanga ngodalira mvula zomwe pano ndi kusintha kwa nyengo zinthu sizikuyenda, sitingapitirire kukhala choncho ngati dziko, tikufunika kusintha nkumapangakonso zina pamwamba pa ulimiwu,” anatero a Kabambe.

Iwo anawuza eni mabanki m’dziko muno kuti apereke ndalama kwa anthu omwe ali ndi maganizo a-bwino atsopano kuti apange zinthu zomwe zithandize kukweza chuma cha dziko.

“Kuli achinyamata ambiri amaliza sukulu zaukachenjede, ali ndi nzeru zatsopano koma alibe poyambira, a mabanki awapatse ndalama agwire ntchito asinthe Malawi,” anatero a Kabambe.

Mkulu wa bungwe la Bankers Association of Malawi a Kwanele             Ngwenya anati, iwo akuyesetsa kuti aliyense akhale ndi mwayi wopeza ndalama monga potsitsa chiwongola dzanja pa ndalama zomwe anthu amabwereka komanso popanga kuti ngakhale anthu akumudzi akhale ndi mwayi wopeza ntchito za mabanki.

Dziko la Malawi likudalirabe mbewu ya fodya pachuma chake ngakhale kuti chaka ndi chaka iku-bwerera mmbuyo pazopeza pa msika.