MkwasoNkhani Zina

Kupanga nawo kafukufuku wa zaulimi kukuthandiza alimi ku Balaka

Wolemba: Jenipher CHANGWANDA, Mtolankhani Wapadera

Kutenga nawo gawo pa kafukufuku wa zaulimi akuti kukuthandiza alimi kupeza phindu lochuluka kaamba koti ali-miwa akutha kupeza mayankho pamavuto omwe amakumana nawo pa nkhani ya zaulimi m’madera awo.

Mlembi wa sukulu ya pamunda ya Tikolole Farmer Field School (FFS), a Madalitso Timothy wochokera m’dera la Mfumu yaikulu James, m’boma la Balaka, ndiwo anena izi pomwe sukuluyi ikupanga kafukufuku wofuna kudziwa michere ya mnthaka yoyenera paulimi m’dera lawo. Kafukufuku ameneyu akuchitika pansi pa pulojekiti ya Sustainable Agriculture Productivity Programme Phase II (SAPP II).

A Timothy ati gulu lawo likuchita kafukufuku ameneyu pa munda wa maekala pafupifupi awiri ndipo anaugawa m’magawo anayi ndicholinga chofuna kupeza michere yomwe ingagwire ntchito bwino m’nthaka ya m’derali.

“Munda wathu tinaugawa m’magawo anayi ndipo gawo loyamba tithira manyowa a m’khola ndi fetereza. Gawo lachiwiri tithira manyowa a m’khuti ndi fetereza. Gawo lachitatu tithira manyowa a chikhunzi; ndipo gawo lomaliza tithira fetereza yekha. Manyowa onsewa tinaphunzira mu pulojekitiyi,” anatero a Timothy.

A Jean Kaligo, omwe ndi msu-ngichuma wa Tikolore FFS ati kupatula kupeza mayankho pa mavuto omwe amakumana nawo pa ulimi m’dera lawo, kutenga nawo gawo pa kafukufuku, kukuthandiza alimi kukhala ndi umwini chifukwa zonse zomwe akuphunzira pa sukuluyi amakachitanso zomwezo m’minda mwawo.

Alimi kupanga madonga othandiza kuchepetsa kuthamanga kwa madzi omwe amayambitsa kukokoloka kwa nthaka (Photo Credit: Jenipher Changwanda)

“M’dera lino takhala tikukumana ndi mavuto ambiri kaamba kakusintha kwa nyengo komanso kukokoloka kwa nthaka, zomwe zimachititsa kuti njala idzitivuta. Koma kudzera mu pulojekiti ya SAPP II, tikukhala ndi umwini chifukwa kafukufuku yense tikumapanga nawo; komanso tikupangira konkuno kusiyana ndi kale pomwe alangizi amangobwera ndi upangiri wokonza kale. Pano tikumaona zomwe zikutheka ndi zomwe zisakutheka. Ndipo timatenga zomwe zatheka ndikukapanga chimodzimodzi m’minda yathu,” anatero a Kaligo.

Iwo anapitiriza kunena kuti: “Kupatula kuchita kafukufuku, taphunziranso upangiri wosiyana-siyana waulimi monga m’mene tingakonzere akalozera, kupanga mizere mwandondomeko, komanso kukonza zigwembe ndikuchita ulimi wa mleranthaka.”

Ndipo m’mawu ake, mlangizi wa derali, a Trevor Makaika, ati kuchita kafukufuku pa sukulu za pamunda ndi alimi kukuwachepetsera ntchito chifukwa alimi akuphunzira komanso kuchita nthawi imodzi mwaokha.

“Kupanga kafukufuku pamodzi ndi alimi kukuchepetsa ntchito yathu ya ulangizi. Alimiwa akumatha kupanga ziganizo zabwino panjira yomwe angatsate pomwe akusiyanitsa makulidwe ambewu m’magawo omwe tapanga pakafukufuku. Ntchito yathu ikukhala yosavuta komanso yopepuka chifukwa mafunso omwe alimi amakhala nawo timakhala tikuthandizana ndi alimi omwewo kuyankha,” anatero a Makaika.

Ndipo mkulu wa zaulimi m’boma la Balaka, a David Alli, ati sukulu za pa munda zikuthandiza ntchito yokweza ulimi m’bomali kaamba koti kudzera msukuluzi, zomwe zilipo 24 m’bomali, nthambi ya zaulimi ikusula alimi omwe akumaphunzitsa alimi anzawo (Lead Farmers) m’madera awo.

“Sukulu za ulimi zikuthandiza chifukwa alimi omwe atenga nawo gawo pa kafukufuku wosiyanasiyana m’sukuluzi akumasanduka akazembe omwe akumaphunzitsa anzawo zaulimi wamakono, womwe unduna wa zamalimidwe ukulimbikitsa. Izi zikuthandiza chifukwa alimi ambiri akufikiridwa ndi upangiri munthawi yochepa ndiyoye-nerera,” anatero a Alli.

Alli: Sukulu za ulimi zikuthandiza kwambiri alimi athu (Photo Credit: Jenipher Changwanda)

A Alli anapitirira kunena kuti sukulu za ulimi zikuthandiza chifukwa magulu alimi ambiri omwe ayamba ngati sukulu za pamunda, akumakhala ma koparetivi zomwe zikuthandiza kutukula miyoyo yawo.

“Chifukwa cha upangiri wa ulimi womwe akuphunzira m’sukuluzi alimi akumakolola zochuluka, zomwe zikuthandizira kuti apange makoparetivi. Ena mwa alimi athu akumathanso kupeza mwayi wa ndalama (grant) woti apititsire patsogolo ulimi wawo ku mabungwe osiyanasiyana. Mabugwewa akumakhala ndi chidwi chowathandiza chifukwa cha ulimi wa makono womwe adaphunzira m’sukuluzi,” a Alli anatero.

SAPP II, yomwe inayamba chaka cha 2024 ndipo idzatha m’chaka cha 2031, yatsamira kwambiri pa maziko amene pulojekiti ya SAPP inayika. SAPP II ikulimbikitsa alimi kukhala m’ma-gulu, ndi kukolola zochuluka atapeza kale misika yodalirika ya zokolola zawo.

Mwa zina, pulojekitiyi ikulimbikitsa kutenga gawo kwa amayi mu ulimi, kuthandiza alimi kuthana ndi mavuto odza kaamba kakusitha kwa nyengo, kusamalira chilengedwe komanso kuonetsetsa kuti mabanja ali ndi chakudya chokwanira.

Ku Balaka SAPP II ili ndi sukulu za alimi zokwana zisanu ndi imodzi (6), zomwe alimi akupezako maphunziro a ukadaulo wa kafukufuku wa malimidwe ndi ziweto.